पवित्र कुरअानको अर्थको अनुवाद - चेवा अनुवाद : खालिद इब्राहीम बेतियाला ।

رقم الصفحة:close

external-link copy
28 : 6

بَلۡ بَدَا لَهُم مَّا كَانُواْ يُخۡفُونَ مِن قَبۡلُۖ وَلَوۡ رُدُّواْ لَعَادُواْ لِمَا نُهُواْ عَنۡهُ وَإِنَّهُمۡ لَكَٰذِبُونَ

(Sichoncho) koma zawaonekera poyera zomwe adali kubisa kale. Ndipo akadabwezedwa akadabwerezanso kuchita zimene adaletsedwa. Ndithudi iwo ngabodza basi. info
التفاسير:

external-link copy
29 : 6

وَقَالُوٓاْ إِنۡ هِيَ إِلَّا حَيَاتُنَا ٱلدُّنۡيَا وَمَا نَحۡنُ بِمَبۡعُوثِينَ

Akumanena: “Palibe moyo wina koma moyo wathu wa pa dziko lapansi basi. Ndipo ife sitidzaukitsidwanso m’manda.” info
التفاسير:

external-link copy
30 : 6

وَلَوۡ تَرَىٰٓ إِذۡ وُقِفُواْ عَلَىٰ رَبِّهِمۡۚ قَالَ أَلَيۡسَ هَٰذَا بِٱلۡحَقِّۚ قَالُواْ بَلَىٰ وَرَبِّنَاۚ قَالَ فَذُوقُواْ ٱلۡعَذَابَ بِمَا كُنتُمۡ تَكۡفُرُونَ

Ndipo ukadaona (tsiku la chiweruziro) pamene azikaimitsidwa pamaso pa Mbuye wawo nauzidwa: “Kodi ichi sichoona?” (Iwo) nati: “Inde nchoona, tikulumbira Mbuye wathu.” (Allah) adzati: “Lawani chilango chifukwa cha kusakhulupirira kwanu (aneneri a Allah).” info
التفاسير:

external-link copy
31 : 6

قَدۡ خَسِرَ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِلِقَآءِ ٱللَّهِۖ حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَتۡهُمُ ٱلسَّاعَةُ بَغۡتَةٗ قَالُواْ يَٰحَسۡرَتَنَا عَلَىٰ مَا فَرَّطۡنَا فِيهَا وَهُمۡ يَحۡمِلُونَ أَوۡزَارَهُمۡ عَلَىٰ ظُهُورِهِمۡۚ أَلَا سَآءَ مَا يَزِرُونَ

Ndithudi, ataika ndi kuonongeka amene akutsutsa zokumana ndi Allah, mpaka mwadzidzidzi nthawi ya Qiyama itawafikira, adzati: “Ho! Masautso pa ife chifukwa chakusalabadira kwathu za zimenezi, uku iwo atasenza mitolo ya machimo kumisana kwao. Taonani kuipa kwa zomwe akusenza. info
التفاسير:

external-link copy
32 : 6

وَمَا ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَآ إِلَّا لَعِبٞ وَلَهۡوٞۖ وَلَلدَّارُ ٱلۡأٓخِرَةُ خَيۡرٞ لِّلَّذِينَ يَتَّقُونَۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ

Ndipo moyo wadziko lapansi sikanthu, koma ndi masewera ndi chibwana. Koma nyumba yomaliza ndiyabwino koposa, (siyofanana ndi chisangalalo cha pa dziko lapansi) kwa omwe akuopa Allah. Bwanji simuzindikira? info
التفاسير:

external-link copy
33 : 6

قَدۡ نَعۡلَمُ إِنَّهُۥ لَيَحۡزُنُكَ ٱلَّذِي يَقُولُونَۖ فَإِنَّهُمۡ لَا يُكَذِّبُونَكَ وَلَٰكِنَّ ٱلظَّٰلِمِينَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ يَجۡحَدُونَ

Ndithu tikudziwa kuti zikukudandaulitsa zomwe akukunenera (pokunyoza ndi kukuyesa wabodza. Ndithu iwo sakukutsutsa iwe; koma oipawa akutsutsa zizindikiro za Allah. info
التفاسير:

external-link copy
34 : 6

وَلَقَدۡ كُذِّبَتۡ رُسُلٞ مِّن قَبۡلِكَ فَصَبَرُواْ عَلَىٰ مَا كُذِّبُواْ وَأُوذُواْ حَتَّىٰٓ أَتَىٰهُمۡ نَصۡرُنَاۚ وَلَا مُبَدِّلَ لِكَلِمَٰتِ ٱللَّهِۚ وَلَقَدۡ جَآءَكَ مِن نَّبَإِيْ ٱلۡمُرۡسَلِينَ

Ndithudi, atumiki onse adatsutsidwa iwe usadadze. Koma adapirira ku zomwe adatsutsidwa, ndipo adazunzidwa kufikira pamene chipulumutso Chathu chidawafika. Palibe wosintha mawu a Allah. Ndithu zakufika nkhani za atumiki (momwe muli malingaliro ndi maphunziro ambiri). info
التفاسير:

external-link copy
35 : 6

وَإِن كَانَ كَبُرَ عَلَيۡكَ إِعۡرَاضُهُمۡ فَإِنِ ٱسۡتَطَعۡتَ أَن تَبۡتَغِيَ نَفَقٗا فِي ٱلۡأَرۡضِ أَوۡ سُلَّمٗا فِي ٱلسَّمَآءِ فَتَأۡتِيَهُم بِـَٔايَةٖۚ وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ لَجَمَعَهُمۡ عَلَى ٱلۡهُدَىٰۚ فَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡجَٰهِلِينَ

Ndipo ngati nkovuta kwa iwe kudzipatula kwawoku (ndi zomwe wadza nazozi pomwe iwo akukuumiriza kuti uwabweretsere chozizwitsa, nawe nkumafuna; zikadatero, pomwe Ine sindikufuna), choncho ngati uli wokhoza kufunafuna njira ya pansi penipeni m’nthaka (kukafuna zozizwitsazo), kapena (ungathe kupeza) makwelero nkukwera kumwamba nkubwera ndi chozizwitsa (chimene akufuna, chita). Allah Akadafuna akadawasonkhanitsa onse ku chiwongoko. Choncho, usakhale mwa osazindikira zinthu. info
التفاسير: