पवित्र कुरअानको अर्थको अनुवाद - चेवा अनुवाद : खालिद इब्राहीम बेतियाला ।

At-Tûr

external-link copy
1 : 52

وَٱلطُّورِ

Ndikulumbilira phiri la Turi (ku Sinai pamene Mûsa adalankhulana ndi Allah). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 52

وَكِتَٰبٖ مَّسۡطُورٖ

Ndi buku lolembedwa. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 52

فِي رَقّٖ مَّنشُورٖ

M’mipukutu yazikopa zotambasuka (zosavuta kuwerenga). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 52

وَٱلۡبَيۡتِ ٱلۡمَعۡمُورِ

Ndi nyumba yopitako kawirikawiri (pochitamo mapemphero). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 52

وَٱلسَّقۡفِ ٱلۡمَرۡفُوعِ

Ndi thambo limene latukulidwa (popanda mzati). info
التفاسير:

external-link copy
6 : 52

وَٱلۡبَحۡرِ ٱلۡمَسۡجُورِ

Ndi nyanja yodzadza ndi madzi. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 52

إِنَّ عَذَابَ رَبِّكَ لَوَٰقِعٞ

Ndithu chilango cha Mbuye wako (chimene wawalonjeza nacho osakhulupirira) chiwapeza (popanda chipeneko). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 52

مَّا لَهُۥ مِن دَافِعٖ

Palibe wochichotsa (pa iwo). info
التفاسير:

external-link copy
9 : 52

يَوۡمَ تَمُورُ ٱلسَّمَآءُ مَوۡرٗا

Pa tsikulo thambo lidzagwedezeka; kugwedezeka kwamphamvu. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 52

وَتَسِيرُ ٱلۡجِبَالُ سَيۡرٗا

Ndipo mapiri adzayenda mwamphavu (kuchoka m’malo mwake). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 52

فَوَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Kuonongeka koopsa pa tsiku limenelo kuzakhala pa otsutsa choonadi. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 52

ٱلَّذِينَ هُمۡ فِي خَوۡضٖ يَلۡعَبُونَ

Iwo amene akungosewera mzinthu zopanda pake. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 52

يَوۡمَ يُدَعُّونَ إِلَىٰ نَارِ جَهَنَّمَ دَعًّا

Tsiku limene adzakankhidwira mwamphamvu ku Jahannam (ku Moto Woopsa). info
التفاسير:

external-link copy
14 : 52

هَٰذِهِ ٱلنَّارُ ٱلَّتِي كُنتُم بِهَا تُكَذِّبُونَ

(Kudzanenedwa kwa iwo): “Uwu ndi Moto uja umene mudali kuutsutsa (pa dziko lapansi) info
التفاسير:

external-link copy
15 : 52

أَفَسِحۡرٌ هَٰذَآ أَمۡ أَنتُمۡ لَا تُبۡصِرُونَ

Kodi awa ndi matsenga kapena inu simukuona? info
التفاسير:

external-link copy
16 : 52

ٱصۡلَوۡهَا فَٱصۡبِرُوٓاْ أَوۡ لَا تَصۡبِرُواْ سَوَآءٌ عَلَيۡكُمۡۖ إِنَّمَا تُجۡزَوۡنَ مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ

Lowanimo, (mulawe kupsereza kwake) pirirani (ndi mavuto ake) kapena musapirire, ndichimodzimodzi kwa inu. Ndithu mulipidwa pazimene munkachita.” info
التفاسير:

external-link copy
17 : 52

إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي جَنَّٰتٖ وَنَعِيمٖ

Ndithu oopa Allah adzakhala m’Minda yamtendere ndi chisangalalo chachikulu. info
التفاسير:

external-link copy
18 : 52

فَٰكِهِينَ بِمَآ ءَاتَىٰهُمۡ رَبُّهُمۡ وَوَقَىٰهُمۡ رَبُّهُمۡ عَذَابَ ٱلۡجَحِيمِ

Uku akukondwelera pazimene wawapatsa Mbuye wawo ndipo Mbuye wawo azawatchinjiriza ku chilango cha Jahena. info
التفاسير:

external-link copy
19 : 52

كُلُواْ وَٱشۡرَبُواْ هَنِيٓـَٔۢا بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ

(Kudzanenedwa kwa iwo): “Idyani (chakudya chamtendere); ndipo imwani mosangalala kukhala malipiro pazimene munkachita (pa dziko lapansi).” info
التفاسير:

external-link copy
20 : 52

مُتَّكِـِٔينَ عَلَىٰ سُرُرٖ مَّصۡفُوفَةٖۖ وَزَوَّجۡنَٰهُم بِحُورٍ عِينٖ

Uku atakhala moyadzamira pa makama ondandika bwino ndi kuyalidwa bwino; ndipo tidzawakwatitsa akazi ophanuka maso mokongola. info
التفاسير:

external-link copy
21 : 52

وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَٱتَّبَعَتۡهُمۡ ذُرِّيَّتُهُم بِإِيمَٰنٍ أَلۡحَقۡنَا بِهِمۡ ذُرِّيَّتَهُمۡ وَمَآ أَلَتۡنَٰهُم مِّنۡ عَمَلِهِم مِّن شَيۡءٖۚ كُلُّ ٱمۡرِيِٕۭ بِمَا كَسَبَ رَهِينٞ

Ndipo amene akhulupirira ndipo ana awo nkuwatsatira pa chikhulupiliro tidzawakumanitsa iwo ndi ana awowo ndipo sitikawachepetsera kalikonse m’mphoto za ntchito zawo; munthu aliyense adzakoledwa ndi zochita zake; info
التفاسير:

external-link copy
22 : 52

وَأَمۡدَدۡنَٰهُم بِفَٰكِهَةٖ وَلَحۡمٖ مِّمَّا يَشۡتَهُونَ

Ndipo tidzawaonjezera zipatso ndi nyama imene adzakhala akuilakalaka. info
التفاسير:

external-link copy
23 : 52

يَتَنَٰزَعُونَ فِيهَا كَأۡسٗا لَّا لَغۡوٞ فِيهَا وَلَا تَأۡثِيمٞ

Azikalandirana m’menemo (mwachikondi wina ndi mnzake) chikho chodzaza ndi zakumwa; sipakakhala kwa iwo zolankhula zachabe ngakhale zochita zamachimo. info
التفاسير:

external-link copy
24 : 52

۞ وَيَطُوفُ عَلَيۡهِمۡ غِلۡمَانٞ لَّهُمۡ كَأَنَّهُمۡ لُؤۡلُؤٞ مَّكۡنُونٞ

Ndipo azikawazungulira anyamata owatumikira onga ngale yosungidwa m’chigoba chake (kukongola kwawo). info
التفاسير:

external-link copy
25 : 52

وَأَقۡبَلَ بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖ يَتَسَآءَلُونَ

Azidzatembenukirana wina ndi mnzake uku akufunsana (za kukula kwa mtendere umene adzakhala nawo ndi kuti adaupeza chotani). info
التفاسير:

external-link copy
26 : 52

قَالُوٓاْ إِنَّا كُنَّا قَبۡلُ فِيٓ أَهۡلِنَا مُشۡفِقِينَ

Adzanena: “Ife tidali oopa chilango cha Allah pakati pa maanja athu (tisadalandire mtenderewu). info
التفاسير:

external-link copy
27 : 52

فَمَنَّ ٱللَّهُ عَلَيۡنَا وَوَقَىٰنَا عَذَابَ ٱلسَّمُومِ

Ndipo Allah watidalitsa ndipo watitchinjiriza ku chilango cha Moto. info
التفاسير:

external-link copy
28 : 52

إِنَّا كُنَّا مِن قَبۡلُ نَدۡعُوهُۖ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡبَرُّ ٱلرَّحِيمُ

Ndithu ife timampembedza (kalero pa dziko lapansi) ndithu Iye Yekha Ngwabwino, Ngwachifundo.” info
التفاسير:

external-link copy
29 : 52

فَذَكِّرۡ فَمَآ أَنتَ بِنِعۡمَتِ رَبِّكَ بِكَاهِنٖ وَلَا مَجۡنُونٍ

Choncho kumbutsa, iwe suli mlosi kapena wamisala pamtendere wa Mbuye wako. info
التفاسير:

external-link copy
30 : 52

أَمۡ يَقُولُونَ شَاعِرٞ نَّتَرَبَّصُ بِهِۦ رَيۡبَ ٱلۡمَنُونِ

Kapena akunena kuti ndiwe mlakatuli, tikumuyembekezera imfa impeze. info
التفاسير:

external-link copy
31 : 52

قُلۡ تَرَبَّصُواْ فَإِنِّي مَعَكُم مِّنَ ٱلۡمُتَرَبِّصِينَ

Nena: “Yembekezerani! Ndithu ine ndili nanu mwa mmodzi woyembekezera.” info
التفاسير:

external-link copy
32 : 52

أَمۡ تَأۡمُرُهُمۡ أَحۡلَٰمُهُم بِهَٰذَآۚ أَمۡ هُمۡ قَوۡمٞ طَاغُونَ

Kapena nzeru zawo ndizo zikuwauza izi kapena iwo ndi anthu opyola malire. info
التفاسير:

external-link copy
33 : 52

أَمۡ يَقُولُونَ تَقَوَّلَهُۥۚ بَل لَّا يُؤۡمِنُونَ

Kodi akunena kuti: “Wadzipekera (Mtumiki {s.a.w} Qur’an)?” Iyayi, koma iwo sakukhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
34 : 52

فَلۡيَأۡتُواْ بِحَدِيثٖ مِّثۡلِهِۦٓ إِن كَانُواْ صَٰدِقِينَ

Tero abwere ndi nkhani yofanana ndi iyo (Qur’an) ngati ali owona m’kuyankhula kwawo (koti Mtumiki{s.a.w} wapeka Qur’an.) info
التفاسير:

external-link copy
35 : 52

أَمۡ خُلِقُواْ مِنۡ غَيۡرِ شَيۡءٍ أَمۡ هُمُ ٱلۡخَٰلِقُونَ

Kapena adalengedwa popanda Mlengi kapena iwo adadzilenga okha (nchifukwa sakuvomereza za Mlengi Wopembedzedwayo?) info
التفاسير:

external-link copy
36 : 52

أَمۡ خَلَقُواْ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَۚ بَل لَّا يُوقِنُونَ

Kapena ndiwo adalenga thambo ndi nthaka? Koma satsimikiza (zoyenera kumchitira Mlengi). info
التفاسير:

external-link copy
37 : 52

أَمۡ عِندَهُمۡ خَزَآئِنُ رَبِّكَ أَمۡ هُمُ ٱلۡمُصَۜيۡطِرُونَ

Kapena nkhokwe (za zabwino) za Mbuye wako zili ndi iwo (kotero kuti akuzigwiritsa ntchito mmene angafunire?) Kapena iwo ngopambana? info
التفاسير:

external-link copy
38 : 52

أَمۡ لَهُمۡ سُلَّمٞ يَسۡتَمِعُونَ فِيهِۖ فَلۡيَأۡتِ مُسۡتَمِعُهُم بِسُلۡطَٰنٖ مُّبِينٍ

Nanga kapena ali nawo makwelero (amene akukwelera kumwamba) kotero kuti akumvetsera zimene Allah akulamula? Choncho, omvetsera awo abwere nawo umboni owonekera (osonyeza kuona kwawo pa zimene akunenazi). info
التفاسير:

external-link copy
39 : 52

أَمۡ لَهُ ٱلۡبَنَٰتُ وَلَكُمُ ٱلۡبَنُونَ

Kapena Iye (Allah) ndiye ali ndi ana akazi ndipo inu muli ndi ana amuna? info
التفاسير:

external-link copy
40 : 52

أَمۡ تَسۡـَٔلُهُمۡ أَجۡرٗا فَهُم مِّن مَّغۡرَمٖ مُّثۡقَلُونَ

Kapena ukuwapempha malipiro alionse (pofikitsa uthenga); kotero kuti iwo akulemedwa ndi kulipira (uthengawu)? info
التفاسير:

external-link copy
41 : 52

أَمۡ عِندَهُمُ ٱلۡغَيۡبُ فَهُمۡ يَكۡتُبُونَ

Kapena iwo amadziwa zamseri kotero kuti iwo akumalemba (zimene afuna)? info
التفاسير:

external-link copy
42 : 52

أَمۡ يُرِيدُونَ كَيۡدٗاۖ فَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ هُمُ ٱلۡمَكِيدُونَ

Kapena akufuna kukuchitira chiwembu (ndikuononga uthenga wako?) Koma amene sadakhulupirire ndiwo omwe chiwabwelere chiwembu (chawo.) info
التفاسير:

external-link copy
43 : 52

أَمۡ لَهُمۡ إِلَٰهٌ غَيۡرُ ٱللَّهِۚ سُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ عَمَّا يُشۡرِكُونَ

Kodi ali naye wompembedza, osati Allah (amene angawateteze ku chilango cha Allah)? Allah wapatukana ndi zimene akumuphatikiza nazo. info
التفاسير:

external-link copy
44 : 52

وَإِن يَرَوۡاْ كِسۡفٗا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ سَاقِطٗا يَقُولُواْ سَحَابٞ مَّرۡكُومٞ

Koma akaona gawo lathambo likugwa (kuti liwalange) akunena (mwamakani ndi kunyada): “Uwu ndi mtambo umene wasonkhanitsa madzi a mvula.” info
التفاسير:

external-link copy
45 : 52

فَذَرۡهُمۡ حَتَّىٰ يُلَٰقُواْ يَوۡمَهُمُ ٱلَّذِي فِيهِ يُصۡعَقُونَ

Choncho asiye; (usalabadire za iwo) mpaka pomwe adzakumana ndi tsiku lawo limene adzaonongedwa. info
التفاسير:

external-link copy
46 : 52

يَوۡمَ لَا يُغۡنِي عَنۡهُمۡ كَيۡدُهُمۡ شَيۡـٔٗا وَلَا هُمۡ يُنصَرُونَ

Tsiku lomwe chiwembu chawo sichidzawathandiza chilichonse; ndipo iwo sadzapulumutsidwa. info
التفاسير:

external-link copy
47 : 52

وَإِنَّ لِلَّذِينَ ظَلَمُواْ عَذَابٗا دُونَ ذَٰلِكَ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ

Ndipo ndithu amene achita zosalungama ali nacho chilango china chosakhala chimenecho (chisanawapeze chilango cha ku Âkhira)! Koma ambiri a iwo sadziwa (zimenezi). info
التفاسير:

external-link copy
48 : 52

وَٱصۡبِرۡ لِحُكۡمِ رَبِّكَ فَإِنَّكَ بِأَعۡيُنِنَاۖ وَسَبِّحۡ بِحَمۡدِ رَبِّكَ حِينَ تَقُومُ

Ndipo pirira ndi lamulo la Mbuye wako ndithu iwe ndiwe wosungidwa ndi kuyang’aniridwa ndi Ife; ndipo lemekeza ndi kumuyamika Mbuye ako pamene ukuimilira (kupemphera). info
التفاسير:

external-link copy
49 : 52

وَمِنَ ٱلَّيۡلِ فَسَبِّحۡهُ وَإِدۡبَٰرَ ٱلنُّجُومِ

Ndipo m’gawo la usiku mlemekeze Iye ndi nthawi yolowa nyenyezi. info
التفاسير: