[14] Ibunu Abbas adati ndime iyi ikufotokoza za atsogoleri a Chiyuda monga Kaabi bun Ashirafi ndi Maliki bun Swaifi ndi Huyaye bun Akhatwabi. Anthuwa adali kulandira mphatso zambiri zochokera kwa anthu awo owatsatira. Pamene Muhammad (s.a.w) adampatsa uneneri iwo sadakhulupirire chifukwa choopa kuti sapeza mitulo yochokera kwa anthu awo. Tero anabisa kwa anthu za uneneri wa Muhammad (s.a.w). Apa mpamene Allah adavumbulutsa Ayah (ndime) iyi, yakuti “Ndithudi, amene akubisa zomwe Allah adavumbulutsa m’buku (la Baibulo) m’malo mwake nasankha zinthu za mtengo wochepa iwo sadya china m’mimba mwawo koma moto basi.”