पवित्र कुरअानको अर्थको अनुवाद - चेवा अनुवाद : खालिद इब्राहीम बेतियाला ।

رقم الصفحة:close

external-link copy
50 : 17

۞ قُلۡ كُونُواْ حِجَارَةً أَوۡ حَدِيدًا

Nena: “Khalani miyala kapena zitsulo.” info
التفاسير:

external-link copy
51 : 17

أَوۡ خَلۡقٗا مِّمَّا يَكۡبُرُ فِي صُدُورِكُمۡۚ فَسَيَقُولُونَ مَن يُعِيدُنَاۖ قُلِ ٱلَّذِي فَطَرَكُمۡ أَوَّلَ مَرَّةٖۚ فَسَيُنۡغِضُونَ إِلَيۡكَ رُءُوسَهُمۡ وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هُوَۖ قُلۡ عَسَىٰٓ أَن يَكُونَ قَرِيبٗا

“Kapena cholengedwa chilichonse mwa zomwe zikuoneka kuti nzovuta kwambiri m’mitima mwanu (m’maganizo mwanu), (ngakhale mutakhala zimenezo, mudzaukitsidwa).” Pamenepo anena: “Ndani adzatibweza?” Nena: “Yemwe adakulengani pachiyambi.” Pamenepo adzakupukusira mitu yawo ndi kunena: “Zichitika liti zimenezo?” Nena: “Mwina zili pafupi!” info
التفاسير:

external-link copy
52 : 17

يَوۡمَ يَدۡعُوكُمۡ فَتَسۡتَجِيبُونَ بِحَمۡدِهِۦ وَتَظُنُّونَ إِن لَّبِثۡتُمۡ إِلَّا قَلِيلٗا

“(Zidzakhala) pa tsiku lomwe adzakuitanani (Allah), ndipo inu mudzayankha momuyamikira, ndipo mudzaganizira kuti simudakhale (pa dziko lapansi) koma (kwa) nthawi yochepa.” info
التفاسير:

external-link copy
53 : 17

وَقُل لِّعِبَادِي يَقُولُواْ ٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُۚ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ يَنزَغُ بَيۡنَهُمۡۚ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ كَانَ لِلۡإِنسَٰنِ عَدُوّٗا مُّبِينٗا

Ndipo auze akapolo Anga kuti (nthawi zonse) azinena zomwe zili zabwino; chifukwa satana amakhwirizira mikangano pakati pawo; ndithu satana kwa munthu, ndi m’dani woonekera. info
التفاسير:

external-link copy
54 : 17

رَّبُّكُمۡ أَعۡلَمُ بِكُمۡۖ إِن يَشَأۡ يَرۡحَمۡكُمۡ أَوۡ إِن يَشَأۡ يُعَذِّبۡكُمۡۚ وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ عَلَيۡهِمۡ وَكِيلٗا

Mbuye wanu akukudziwani bwino. Ngati afuna akuchitirani chisoni (mukatembenukira kwa Iye), ndipo ngati afuna, akulangani (mukapitiriza kumnyoza); ndipo sitidakutumize kuti ukhale muyang’anili wawo. info
التفاسير:

external-link copy
55 : 17

وَرَبُّكَ أَعۡلَمُ بِمَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۗ وَلَقَدۡ فَضَّلۡنَا بَعۡضَ ٱلنَّبِيِّـۧنَ عَلَىٰ بَعۡضٖۖ وَءَاتَيۡنَا دَاوُۥدَ زَبُورٗا

Ndipo Mbuye wako akuwadziwa bwino onse ali kumwamba ndi pansi, ndithu tawapatsa ulemelero wambiri aneneri ena kuposa ena. Ndipo Daud tidampatsa Zaburi. info
التفاسير:

external-link copy
56 : 17

قُلِ ٱدۡعُواْ ٱلَّذِينَ زَعَمۡتُم مِّن دُونِهِۦ فَلَا يَمۡلِكُونَ كَشۡفَ ٱلضُّرِّ عَنكُمۡ وَلَا تَحۡوِيلًا

Nena: “Aitaneni amene mukuwatcha kuti ndi milungu kusiya Iye (Allah) kuti akuchotsereni masautso, sadzatha kukuchotserani vuto lililonse ngakhale kulisintha (kuti likhale chabwino).” info
التفاسير:

external-link copy
57 : 17

أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ يَبۡتَغُونَ إِلَىٰ رَبِّهِمُ ٱلۡوَسِيلَةَ أَيُّهُمۡ أَقۡرَبُ وَيَرۡجُونَ رَحۡمَتَهُۥ وَيَخَافُونَ عَذَابَهُۥٓۚ إِنَّ عَذَابَ رَبِّكَ كَانَ مَحۡذُورٗا

Iwo amene akuwapempha (naonso) akufunafuna njira yoziyandikitsira kwa Mbuye wawo (ngakhale) omwe ali pafupi mwa iwo (ndi Allah, monga angelo); naonso akuyembekezera chifundo chake ndi kuopa chilango chake; ndithu chilango cha Mbuye wako, nchoopedwa. info
التفاسير:

external-link copy
58 : 17

وَإِن مِّن قَرۡيَةٍ إِلَّا نَحۡنُ مُهۡلِكُوهَا قَبۡلَ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ أَوۡ مُعَذِّبُوهَا عَذَابٗا شَدِيدٗاۚ كَانَ ذَٰلِكَ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مَسۡطُورٗا

Ndipo sipadzapezeka mudzi uliwonse koma Ife tidzauphwasula tsiku la Qiyâma lisanadze, kapena tidzaulanga ndi chilango chaukali (ngati uli woyenerana ndi zimenezo). Izi zidalembedwa m’buku. info
التفاسير: