വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ വിവർത്തനം - ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബറ്റിയാലാ

പേജ് നമ്പർ:close

external-link copy
119 : 6

وَمَا لَكُمۡ أَلَّا تَأۡكُلُواْ مِمَّا ذُكِرَ ٱسۡمُ ٱللَّهِ عَلَيۡهِ وَقَدۡ فَصَّلَ لَكُم مَّا حَرَّمَ عَلَيۡكُمۡ إِلَّا مَا ٱضۡطُرِرۡتُمۡ إِلَيۡهِۗ وَإِنَّ كَثِيرٗا لَّيُضِلُّونَ بِأَهۡوَآئِهِم بِغَيۡرِ عِلۡمٍۚ إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعۡلَمُ بِٱلۡمُعۡتَدِينَ

Mungasiirenji kudya (nyama) imene poizinga dzina la Allah latchulidwapo, pomwe wakufotokozerani momveka chomwe wachiletsa kwa inu, kupatula (mukadya choletsedwacho) mosimidwa ndi kukakamizidwa (chifukwa cha njala)? Koma ndithu ambiri akusokeretsa (ena) mwa zifuniro zawo popanda kudziwa. Ndithu Mbuye wako ndi Yemwe akudziwa bwino za olumpha malire. info
التفاسير:

external-link copy
120 : 6

وَذَرُواْ ظَٰهِرَ ٱلۡإِثۡمِ وَبَاطِنَهُۥٓۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ يَكۡسِبُونَ ٱلۡإِثۡمَ سَيُجۡزَوۡنَ بِمَا كَانُواْ يَقۡتَرِفُونَ

Siyani machimo oonekera ndi obisika. Ndithu amene achita machimo adzalipidwa chifukwa cha zomwe adali kuchita (zoipa). info
التفاسير:

external-link copy
121 : 6

وَلَا تَأۡكُلُواْ مِمَّا لَمۡ يُذۡكَرِ ٱسۡمُ ٱللَّهِ عَلَيۡهِ وَإِنَّهُۥ لَفِسۡقٞۗ وَإِنَّ ٱلشَّيَٰطِينَ لَيُوحُونَ إِلَىٰٓ أَوۡلِيَآئِهِمۡ لِيُجَٰدِلُوكُمۡۖ وَإِنۡ أَطَعۡتُمُوهُمۡ إِنَّكُمۡ لَمُشۡرِكُونَ

Ndipo musadye (nyama) imene yazingidwa popanda kutchula dzina la Allah. Kutero ndikuchimwa. Ndithudi, asatana amanong’onezera abwenzi awo kuti akangane ndi inu (m’zinthu zonga zimenezi). Ngati muwamvera, ndiye kuti mukhala opembedza mafano. info
التفاسير:

external-link copy
122 : 6

أَوَمَن كَانَ مَيۡتٗا فَأَحۡيَيۡنَٰهُ وَجَعَلۡنَا لَهُۥ نُورٗا يَمۡشِي بِهِۦ فِي ٱلنَّاسِ كَمَن مَّثَلُهُۥ فِي ٱلظُّلُمَٰتِ لَيۡسَ بِخَارِجٖ مِّنۡهَاۚ كَذَٰلِكَ زُيِّنَ لِلۡكَٰفِرِينَ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Kodi yemwe adali wakufa, kenako nkumuukitsa ndi kumpangira kuunika; choncho ndi kuunikako nkumayenda kwa anthu, kodi angafanane ndi yemwe chikhalidwe chake chili mu mdima (wa umbuli) ndipo sakutha kutuluka m’menemo? Motero zakometsedwa kwa osakhulupirira (zoipa) zomwe akhala akuchita. info
التفاسير:

external-link copy
123 : 6

وَكَذَٰلِكَ جَعَلۡنَا فِي كُلِّ قَرۡيَةٍ أَكَٰبِرَ مُجۡرِمِيهَا لِيَمۡكُرُواْ فِيهَاۖ وَمَا يَمۡكُرُونَ إِلَّا بِأَنفُسِهِمۡ وَمَا يَشۡعُرُونَ

Chomwechonso tidaika mmudzi uli wonse akuluakulu owonongamo kuti azichitamo ndale (zoletsa anthu kuyenda pa njira ya Allah). Ndipo ndale zawo sizipweteka aliyense koma iwo eni, koma sazindikira. info
التفاسير:

external-link copy
124 : 6

وَإِذَا جَآءَتۡهُمۡ ءَايَةٞ قَالُواْ لَن نُّؤۡمِنَ حَتَّىٰ نُؤۡتَىٰ مِثۡلَ مَآ أُوتِيَ رُسُلُ ٱللَّهِۘ ٱللَّهُ أَعۡلَمُ حَيۡثُ يَجۡعَلُ رِسَالَتَهُۥۗ سَيُصِيبُ ٱلَّذِينَ أَجۡرَمُواْ صَغَارٌ عِندَ ٱللَّهِ وَعَذَابٞ شَدِيدُۢ بِمَا كَانُواْ يَمۡكُرُونَ

Ndipo chizindikiro chikawadzera, amati: “Sitikhulupirira, mpaka tipatsidwe monga zomwe atumiki a Allah adapatsidwa.” Allah ndiamene akudziwa pamalo pomwe akuika uneneri Wake, (sikuti angapatsidwe munthu aliyense). Posachedwa kunyozeka kochokera kwa Allah ndi chilango choopsa ziwafika amene achita zoipa chifukwa cha ndale zawo zomwe akhala akuchita. info
التفاسير: