വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ വിവർത്തനം - ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബറ്റിയാലാ

Qâf

external-link copy
1 : 50

قٓۚ وَٱلۡقُرۡءَانِ ٱلۡمَجِيدِ

Qaf. Ndikulumbira Qur’an yolemekezeka. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 50

بَلۡ عَجِبُوٓاْ أَن جَآءَهُم مُّنذِرٞ مِّنۡهُمۡ فَقَالَ ٱلۡكَٰفِرُونَ هَٰذَا شَيۡءٌ عَجِيبٌ

Koma akudabwa chifukwa chowadzera Mchenjezi wochokera mwa iwo. Ndipo osakhulupirira adanena: “Ichi nchinthu chodabwitsa.” info
التفاسير:

external-link copy
3 : 50

أَءِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابٗاۖ ذَٰلِكَ رَجۡعُۢ بَعِيدٞ

Kodi tikadzafa ndi kukhala fumbi (tidzaukanso?) Kubwerera kumeneko nkwakutali kwambiri, (nkosatheka).” info
التفاسير:

external-link copy
4 : 50

قَدۡ عَلِمۡنَا مَا تَنقُصُ ٱلۡأَرۡضُ مِنۡهُمۡۖ وَعِندَنَا كِتَٰبٌ حَفِيظُۢ

Ndithu tikudziwa chimene nthaka ikuchepetsa m’matupi mwawo (akalowa m’manda). Ndipo kwa Ife kuli kaundula wosungidwa. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 50

بَلۡ كَذَّبُواْ بِٱلۡحَقِّ لَمَّا جَآءَهُمۡ فَهُمۡ فِيٓ أَمۡرٖ مَّرِيجٍ

Koma adatsutsa choona pamene chidawadzera. Ndipo iwo ali m’chinthu chosokonezeka. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 50

أَفَلَمۡ يَنظُرُوٓاْ إِلَى ٱلسَّمَآءِ فَوۡقَهُمۡ كَيۡفَ بَنَيۡنَٰهَا وَزَيَّنَّٰهَا وَمَا لَهَا مِن فُرُوجٖ

Kodi sawona thambo pamwamba pawo m’mene tidalimangira ndi kulikongoletsa? Ndipo lilibe ming’alu? info
التفاسير:

external-link copy
7 : 50

وَٱلۡأَرۡضَ مَدَدۡنَٰهَا وَأَلۡقَيۡنَا فِيهَا رَوَٰسِيَ وَأَنۢبَتۡنَا فِيهَا مِن كُلِّ زَوۡجِۭ بَهِيجٖ

Ndipo nthaka tidaiyala; ndi kuika mapiri m’menemo ndi kumeretsamo m’mera Wokongola wamtundu uliwonse. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 50

تَبۡصِرَةٗ وَذِكۡرَىٰ لِكُلِّ عَبۡدٖ مُّنِيبٖ

(Kuti zimenezi zikhale) chotsekula maso ndi chikumbutso kwa munthu aliyense wotembenukira (kwa Allah). info
التفاسير:

external-link copy
9 : 50

وَنَزَّلۡنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ مُّبَٰرَكٗا فَأَنۢبَتۡنَا بِهِۦ جَنَّٰتٖ وَحَبَّ ٱلۡحَصِيدِ

Ndipo tatsitsa madzi odalitsidwa kuchokera ku mitambo, ndipo kupyolera m’madziwo, tameretsa (mmera) m’minda ndi mbewu zokololedwa. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 50

وَٱلنَّخۡلَ بَاسِقَٰتٖ لَّهَا طَلۡعٞ نَّضِيدٞ

Ndi mitengo italiitali ya kanjedza yokhala ndi mikoko yazipatso zothothana. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 50

رِّزۡقٗا لِّلۡعِبَادِۖ وَأَحۡيَيۡنَا بِهِۦ بَلۡدَةٗ مَّيۡتٗاۚ كَذَٰلِكَ ٱلۡخُرُوجُ

(Kuti chikhale) chakudya cha akapolo (a Allah); ndi madziwo taukitsa dziko lakufa (louma). Momwemo ndimmene kudzakhalira kutuluka m’manda (muli moyo). info
التفاسير:

external-link copy
12 : 50

كَذَّبَتۡ قَبۡلَهُمۡ قَوۡمُ نُوحٖ وَأَصۡحَٰبُ ٱلرَّسِّ وَثَمُودُ

Kale, iwo kulibe, adatsutsa anthu a Nuh ndi eni chitsime ndi Asamudu. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 50

وَعَادٞ وَفِرۡعَوۡنُ وَإِخۡوَٰنُ لُوطٖ

Ndi Âdi, ndi Farawo ndi Abale a Luti. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 50

وَأَصۡحَٰبُ ٱلۡأَيۡكَةِ وَقَوۡمُ تُبَّعٖۚ كُلّٞ كَذَّبَ ٱلرُّسُلَ فَحَقَّ وَعِيدِ

Ndi anthu a m’mitengo (ya Aika), ndi anthu a Tubba; onsewo adatsutsa Aneneri; choncho chenjezo Langa lidatsimikizika (pa iwo). info
التفاسير:

external-link copy
15 : 50

أَفَعَيِينَا بِٱلۡخَلۡقِ ٱلۡأَوَّلِۚ بَلۡ هُمۡ فِي لَبۡسٖ مِّنۡ خَلۡقٖ جَدِيدٖ

Kodi tidatopa nkulenga koyamba? Koma iwo ali m’maganizo osokonezeka m’zakalengedwe katsopano. info
التفاسير: