[113] Apa akufotokoza mmene anthu ena angawagawireko chuma chamasiye.
a) Ngati atafa mkazi nkusiya mwamuna wake yekha popanda kusiya ana kapena adzukulu, mwamunayo alandire gawo limodzi mwa magawo awiri (1/2) a chuma chomwe wasiya mkazi wakecho.
b) Akafa mkazi nkusiya mwamuna ndi nnwana wake kapena mdzukulu wake apa ndiye kuti mwamunayo adzalandira (1/4) gawo limodzi mwa magawo anayi achumacho.
c) Akafa mwamuna nkusiya mkazi wake popanda mwana kapena mdzukulu wake ndiye kuti mkaziyo adzalandira (1/4) gawo limodzi mwamagawo anayi achuma cha mwamuna wakecho. Ndipo chotsalacho achipereke kwa ena ofunika kuwagawira.
d) Akafa mwamuna nkusiya mkazi wake ndi mwana wake kapena mdzukulu wake, apa mkazi alandire (1/8) gawo limodzi mwa magawo asanu ndi atatu a chuma cha mwamunayo.
e) Akamwalira munthu popanda kusiya ana kapena zidzukulu ndi makolo, koma nkusiya m’bale mmodzi wamwamuna kapena wamkazi wakumbali ya mayi, apa ndiye kuti m’baleyo adzalandira (1/6) gawo limodzi mwa magawo asanu ndi limodzi a chumacho. Ndipo chotsalacho adzawagawira ena oyenera kuwagawira ngati alipo. Koma ngati palibe ndiye kuti m’baleyo adzatenganso chotsalacho.
f) Akamwalira munthu popanda kusiya ana kapena adzukulu ndi makolo, koma wasiya abale akumbali yamayi, amuna kapena akazi, apa ndiye kuti abalewa adzalandira (1/3) gawo limodzi mwa magawo atatu achuma cha womwalirayo. Ndipo adzagawana pakati pawo mofanana amuna ndi akazi omwe.