വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ വിവർത്തനം - ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബറ്റിയാലാ

പേജ് നമ്പർ:close

external-link copy
77 : 37

وَجَعَلۡنَا ذُرِّيَّتَهُۥ هُمُ ٱلۡبَاقِينَ

Ndipo tidazichita zidzukulu zake kukhala zotsala (pa dziko, oipa ataonongeka). info
التفاسير:

external-link copy
78 : 37

وَتَرَكۡنَا عَلَيۡهِ فِي ٱلۡأٓخِرِينَ

Ndipo tidamsiira mbiri yabwino kwa mibadwo yodza pambuyo pake. info
التفاسير:

external-link copy
79 : 37

سَلَٰمٌ عَلَىٰ نُوحٖ فِي ٱلۡعَٰلَمِينَ

Mtendere ukhale pa Nuh pa zolengedwa zonse. info
التفاسير:

external-link copy
80 : 37

إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Ndithu umu ndimomwe Ife tilipirira ochita zabwino. info
التفاسير:

external-link copy
81 : 37

إِنَّهُۥ مِنۡ عِبَادِنَا ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Ndithu iye ndi mmodzi mwa akapolo Athu okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
82 : 37

ثُمَّ أَغۡرَقۡنَا ٱلۡأٓخَرِينَ

Kenako tidawamiza enawo. info
التفاسير:

external-link copy
83 : 37

۞ وَإِنَّ مِن شِيعَتِهِۦ لَإِبۡرَٰهِيمَ

Ndipo ndithu m’gulu lake (la Nuh) muli Ibrahim. info
التفاسير:

external-link copy
84 : 37

إِذۡ جَآءَ رَبَّهُۥ بِقَلۡبٖ سَلِيمٍ

Kumbuka pamene adadza kwa Mbuye wake ndi mtima wabwino (wogonjera malamulo). info
التفاسير:

external-link copy
85 : 37

إِذۡ قَالَ لِأَبِيهِ وَقَوۡمِهِۦ مَاذَا تَعۡبُدُونَ

Pomwe adanena kwa bambo wake ndi anthu ake: “Mukupembedza chiyani?” info
التفاسير:

external-link copy
86 : 37

أَئِفۡكًا ءَالِهَةٗ دُونَ ٱللَّهِ تُرِيدُونَ

“Ha! Milungu yopeka kusiya Allah, ndi imene mukuifuna?” info
التفاسير:

external-link copy
87 : 37

فَمَا ظَنُّكُم بِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

“Kodi maganizo anu ngotani pa Mbuye wa zolengedwa zonse?” info
التفاسير:

external-link copy
88 : 37

فَنَظَرَ نَظۡرَةٗ فِي ٱلنُّجُومِ

Ndipo adayang’ana nyenyezi mozama. info
التفاسير:

external-link copy
89 : 37

فَقَالَ إِنِّي سَقِيمٞ

Ndipo adanena: “Ine ndine wodwala!” info
التفاسير:

external-link copy
90 : 37

فَتَوَلَّوۡاْ عَنۡهُ مُدۡبِرِينَ

Choncho iwo adatembenuka ndi kumsiya. info
التفاسير:

external-link copy
91 : 37

فَرَاغَ إِلَىٰٓ ءَالِهَتِهِمۡ فَقَالَ أَلَا تَأۡكُلُونَ

(Ibrahim) adapita mozemba ku mafano awo, ndipo adawauza (mwachipongwe:) “Bwanji simukudya (chakudya chomwe chaikidwa patsogolo panupo)?” info
التفاسير:

external-link copy
92 : 37

مَا لَكُمۡ لَا تَنطِقُونَ

“Bwanji simukuyankhula?” info
التفاسير:

external-link copy
93 : 37

فَرَاغَ عَلَيۡهِمۡ ضَرۡبَۢا بِٱلۡيَمِينِ

Atatero adawatembenukira ndi kuwamenya (mwamphamvu) ndi dzanja lamanja. info
التفاسير:

external-link copy
94 : 37

فَأَقۡبَلُوٓاْ إِلَيۡهِ يَزِفُّونَ

(Pamene adamva eni mafanowo) adadza kwa iye akuthamanga. info
التفاسير:

external-link copy
95 : 37

قَالَ أَتَعۡبُدُونَ مَا تَنۡحِتُونَ

Anati: “Kodi mukupembedza (miyala) imene mwasema?” info
التفاسير:

external-link copy
96 : 37

وَٱللَّهُ خَلَقَكُمۡ وَمَا تَعۡمَلُونَ

“Chikhalirecho Allah ndiye adakulengani ndi zimene mukuchita!” info
التفاسير:

external-link copy
97 : 37

قَالُواْ ٱبۡنُواْ لَهُۥ بُنۡيَٰنٗا فَأَلۡقُوهُ فِي ٱلۡجَحِيمِ

Iwo adati: “Mmangireni ng’anjo, ndipo mponyeni m’motowo.” info
التفاسير:

external-link copy
98 : 37

فَأَرَادُواْ بِهِۦ كَيۡدٗا فَجَعَلۡنَٰهُمُ ٱلۡأَسۡفَلِينَ

Adafuna kumchita chiwembu (kuti amuphe ndi moto), koma tidawachita kukhala onyozeka. info
التفاسير:

external-link copy
99 : 37

وَقَالَ إِنِّي ذَاهِبٌ إِلَىٰ رَبِّي سَيَهۡدِينِ

Ndipo (Ibrahim) adati: “Ndithu ine ndikupita kwa Mbuye wanga, Iye andiongolera.” info
التفاسير:

external-link copy
100 : 37

رَبِّ هَبۡ لِي مِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ

“E Mbuye wanga! Ndipatseni mwana yemwe adzakhale (mmodzi) mwa olungama!” info
التفاسير:

external-link copy
101 : 37

فَبَشَّرۡنَٰهُ بِغُلَٰمٍ حَلِيمٖ

Ndipo tidamuuza nkhani yabwino ya mwana wofatsa, (mwanayo ndi Ismaila). info
التفاسير:

external-link copy
102 : 37

فَلَمَّا بَلَغَ مَعَهُ ٱلسَّعۡيَ قَالَ يَٰبُنَيَّ إِنِّيٓ أَرَىٰ فِي ٱلۡمَنَامِ أَنِّيٓ أَذۡبَحُكَ فَٱنظُرۡ مَاذَا تَرَىٰۚ قَالَ يَٰٓأَبَتِ ٱفۡعَلۡ مَا تُؤۡمَرُۖ سَتَجِدُنِيٓ إِن شَآءَ ٱللَّهُ مِنَ ٱلصَّٰبِرِينَ

Ndipo (adabadwa ndi kuyamba kukula.) Pamene adakwana nsinkhu woyenda pamodzi ndi tate wake pochitachita za m’dziko (Ibrahim adayesedwa mayeso kupyolera m’maloto omwe adalota). Adati: “E mwana wanga! Ine kutulo ndikuona maloto (owona ochokera kwa Allah omwe akundilamula) kuti ndikuzinge (monga nsembe yopereka kwa Allah). Nanga ukuti bwanji?” (Mwana wabwino) adanena: “Bambo wanga! Kwaniritsani chimene mukulamulidwa. Ngati Allah afuna, mundipeza ndili mmodzi mwa opirira.” info
التفاسير: