വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ വിവർത്തനം - ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബറ്റിയാലാ

പേജ് നമ്പർ:close

external-link copy
33 : 25

وَلَا يَأۡتُونَكَ بِمَثَلٍ إِلَّا جِئۡنَٰكَ بِٱلۡحَقِّ وَأَحۡسَنَ تَفۡسِيرًا

Ndipo sangakubweretsere fanizo lililonse koma tikubweretsera choonadi (choyankha fanizolo ndi kukudziwitsa) ndi kumasulira kwabwino. info
التفاسير:

external-link copy
34 : 25

ٱلَّذِينَ يُحۡشَرُونَ عَلَىٰ وُجُوهِهِمۡ إِلَىٰ جَهَنَّمَ أُوْلَٰٓئِكَ شَرّٞ مَّكَانٗا وَأَضَلُّ سَبِيلٗا

Amene adzasonkhanitsidwe akukokedwa ndi nkhope zawo kunka ku Jahanama, iwowo adzakhala pamalo oipa ndipo ngosokera njira (yachoonadi). info
التفاسير:

external-link copy
35 : 25

وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ وَجَعَلۡنَا مَعَهُۥٓ أَخَاهُ هَٰرُونَ وَزِيرٗا

Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku. Ndipo m’bale wake Harun (Aroni) tidamsankha kukhala nduna (yake). info
التفاسير:

external-link copy
36 : 25

فَقُلۡنَا ٱذۡهَبَآ إِلَى ٱلۡقَوۡمِ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا فَدَمَّرۡنَٰهُمۡ تَدۡمِيرٗا

Choncho tidati: “Pitani kwa anthu omwe atsutsa zisonyezo Zathu. Tero, tidawaononga kotheratu.” info
التفاسير:

external-link copy
37 : 25

وَقَوۡمَ نُوحٖ لَّمَّا كَذَّبُواْ ٱلرُّسُلَ أَغۡرَقۡنَٰهُمۡ وَجَعَلۡنَٰهُمۡ لِلنَّاسِ ءَايَةٗۖ وَأَعۡتَدۡنَا لِلظَّٰلِمِينَ عَذَابًا أَلِيمٗا

Naonso anthu a Nuh, pamene adatsutsa atumiki, tidawamiza, ndipo tidawachita kukhala phunziro kwa anthu, ndipo anthu osalungama tawakonzera chilango chowawa. info
التفاسير:

external-link copy
38 : 25

وَعَادٗا وَثَمُودَاْ وَأَصۡحَٰبَ ٱلرَّسِّ وَقُرُونَۢا بَيۡنَ ذَٰلِكَ كَثِيرٗا

Nawonso Âdi, Asamudu ndi eni chitsime ndi mibadwo yambiri pakati pa iwo. info
التفاسير:

external-link copy
39 : 25

وَكُلّٗا ضَرَبۡنَا لَهُ ٱلۡأَمۡثَٰلَۖ وَكُلّٗا تَبَّرۡنَا تَتۡبِيرٗا

Ndipo onse tidawaponyera mafanizo; ndiponso onse tidawaononga motheratu (pamene adakana kutsatira malamulo athu). info
التفاسير:

external-link copy
40 : 25

وَلَقَدۡ أَتَوۡاْ عَلَى ٱلۡقَرۡيَةِ ٱلَّتِيٓ أُمۡطِرَتۡ مَطَرَ ٱلسَّوۡءِۚ أَفَلَمۡ يَكُونُواْ يَرَوۡنَهَاۚ بَلۡ كَانُواْ لَا يَرۡجُونَ نُشُورٗا

Ndipo ndithu iwo (Aquraish, m’maulendo awo) adafika pa mudzi (Sodomu ndi Gomora) womwe mvula yoipa (ya sangalabwi) idawavumbwa. Kodi sadali kuuona? Koma sadali kuyembekezera zakuuka ku imfa. info
التفاسير:

external-link copy
41 : 25

وَإِذَا رَأَوۡكَ إِن يَتَّخِذُونَكَ إِلَّا هُزُوًا أَهَٰذَا ٱلَّذِي بَعَثَ ٱللَّهُ رَسُولًا

Ndipo akakuona (iwe Mtumiki Muhammad {s.a.w}), amangokuchitira chipongwe: “Kodi uyu ndi yemwe Allah wamtuma kuti akhale mtumiki?” info
التفاسير:

external-link copy
42 : 25

إِن كَادَ لَيُضِلُّنَا عَنۡ ءَالِهَتِنَا لَوۡلَآ أَن صَبَرۡنَا عَلَيۡهَاۚ وَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ حِينَ يَرَوۡنَ ٱلۡعَذَابَ مَنۡ أَضَلُّ سَبِيلًا

“Ndithu adatsala pang’ono kutisokeretsa ku milungu yathu, tikadapanda kupirira pa milunguyo.” Posachedwapa adziwa, pamene adzaona chilango, (kuti) ndani wosokera zedi njira. info
التفاسير:

external-link copy
43 : 25

أَرَءَيۡتَ مَنِ ٱتَّخَذَ إِلَٰهَهُۥ هَوَىٰهُ أَفَأَنتَ تَكُونُ عَلَيۡهِ وَكِيلًا

Kodi wamuona yemwe wachichita chilakolako chake (chimene akuchikonda) kukhala mulungu wake? Kodi iweyo ungathe kukhala muyang’aniri wa iye (kotero kuti ungamkakamize chomwe safuna)? info
التفاسير: