[392] (Ndime 8-9) Ma Ayah awiriwa akufotokoza momwe Aarabu adalili Usilamu usadabwere. Munthu ankati akapatsidwa mphatso ya mwana wa mkazi adali kukhumudwa ndi kudandaula kwambiri. Ankanena kuti asungwana ngopanda phindu ndipo kuti kudali kuononga zinthu pakumulera, kumudyetsa, ndi kumuveka. Ndipo akadzakhala wachiwerewere adzakhala manyazi aakulu kwa makolo ake. Pamene chidadza chisilamu chidathetsa mkhalidwewu. Ndipo apa Allah akutisonyeza kuti patsiku limenelo, la chiweruziro, mwana uja adaikidwa wa moyo, adzafunsidwa kuti adaphedwa ndi tchimo lanji. Iye adzayankha kuti sadachite tchimo lililonse koma adaphedwa mopanda chilungamo.
[393] Awa ndi makalata achiwerengero momwe mwalembedwa zabwino za munthu ndi zoipa zake. Tsiku limenelo munthu aliyense adzapatsidwa yake kalata kuti aone iye mwini zoipa ndi zabwino zake.
[395] (Ndime 19-20) Mthenga wolemekezeka womveredwa uko kumwamba ndi Jibril (Gabriele) yemwe ndi wamkulu wa angelo onse. Iye ndiyemwe adali kubweretsa Qur’an mwa lamulo la Allah kwa Mneneri Wake Muhammad (s.a.w). Ndipo ulemelero wa Qur’an ndi ulemelero wa Mneneri (s.a.w) chifukwa choti munthu wolemekezeka amamutumizira mthenga wolemekezekanso. Ndipo uthenga wabwino umapatsidwa kwa Mneneri wabwino woposa onse.