ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ

Al-Ma’ârij

external-link copy
1 : 70

سَأَلَ سَآئِلُۢ بِعَذَابٖ وَاقِعٖ

Wopempha adapempha kuti chiwadzere msanga chilango chopezekacho, (m’kupempha kwa chipongwe ndi kotsutsa). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 70

لِّلۡكَٰفِرِينَ لَيۡسَ لَهُۥ دَافِعٞ

Kwa okanira palibe angachitsekereze. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 70

مِّنَ ٱللَّهِ ذِي ٱلۡمَعَارِجِ

Chochokera kwa Allah Mwini makwelero. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 70

تَعۡرُجُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ وَٱلرُّوحُ إِلَيۡهِ فِي يَوۡمٖ كَانَ مِقۡدَارُهُۥ خَمۡسِينَ أَلۡفَ سَنَةٖ

Angelo ndi Jiburil amakwera kwa Iye (Allah) m’tsiku lomwe kutalika kwake kuli ngati zaka zikwi makumi asanu (50 000). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 70

فَٱصۡبِرۡ صَبۡرٗا جَمِيلًا

Choncho, pirira (iwe Mtumiki (s.a.w) kupirira kwabwino, info
التفاسير:

external-link copy
6 : 70

إِنَّهُمۡ يَرَوۡنَهُۥ بَعِيدٗا

Ndithu iwo akuliona (tsiku la Qiyâma) kuti lili kutali (silingachitike). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 70

وَنَرَىٰهُ قَرِيبٗا

Koma Ife tikuliona kuti lilipafupi (ndilochitika). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 70

يَوۡمَ تَكُونُ ٱلسَّمَآءُ كَٱلۡمُهۡلِ

Tsiku limene thambo lidzakhala ngati mtovu wosungunuka. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 70

وَتَكُونُ ٱلۡجِبَالُ كَٱلۡعِهۡنِ

Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya (wongouluka wokha). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 70

وَلَا يَسۡـَٔلُ حَمِيمٌ حَمِيمٗا

Ndipo m’bale sadzafunsa za m’bale wake. info
التفاسير: