ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ

ಪುಟ ಸಂಖ್ಯೆ: 160:151 close

external-link copy
82 : 7

وَمَا كَانَ جَوَابَ قَوۡمِهِۦٓ إِلَّآ أَن قَالُوٓاْ أَخۡرِجُوهُم مِّن قَرۡيَتِكُمۡۖ إِنَّهُمۡ أُنَاسٞ يَتَطَهَّرُونَ

Kuyankha kwa anthu ake sikudali kwa mtundu wina koma kuti: “Apirikitseni m’mudzi wanu. Ndithu iwowo ndi anthu odziyeretsa. (Choncho akhaliranji m’mudzi wa uve? Akakhale ndi anzawo ochita zaukhondo).” info
التفاسير:

external-link copy
83 : 7

فَأَنجَيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥٓ إِلَّا ٱمۡرَأَتَهُۥ كَانَتۡ مِنَ ٱلۡغَٰبِرِينَ

Koma tidampulumutsa iye ndi banja lake, kupatula mkazi wake; adali m’gulu la otsalira m’mbuyo (adaonongeka). info
التفاسير:

external-link copy
84 : 7

وَأَمۡطَرۡنَا عَلَيۡهِم مَّطَرٗاۖ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُجۡرِمِينَ

Ndipo tidatsakamula pa iwo chimvula (cha miyala). Choncho, taona mmene adaliri mapeto a anthu oipa. info
التفاسير:

external-link copy
85 : 7

وَإِلَىٰ مَدۡيَنَ أَخَاهُمۡ شُعَيۡبٗاۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥۖ قَدۡ جَآءَتۡكُم بَيِّنَةٞ مِّن رَّبِّكُمۡۖ فَأَوۡفُواْ ٱلۡكَيۡلَ وَٱلۡمِيزَانَ وَلَا تَبۡخَسُواْ ٱلنَّاسَ أَشۡيَآءَهُمۡ وَلَا تُفۡسِدُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ بَعۡدَ إِصۡلَٰحِهَاۚ ذَٰلِكُمۡ خَيۡرٞ لَّكُمۡ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَ

Nakonso kwa anthu aku Madiyan, (tidamtumiza) m’bale wawo Shuaib. Adati: “E inu anthu Anga! Gwadirani Allah. Mulibe mulungu wina koma Iye basi. Umboni owonekera wadza kuchokera kwa Mbuye wanu. Choncho pimani miyeso (yanu ya mbale) ndi masikelo mwachilungamo. Musawachepetsere anthu zinthu zawo; ndipo musaononge pa dziko pamhuyo polikonza. Kutero ndi kwabwino kwa inu ngati muli okhulupiriradi.” info
التفاسير:

external-link copy
86 : 7

وَلَا تَقۡعُدُواْ بِكُلِّ صِرَٰطٖ تُوعِدُونَ وَتَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ مَنۡ ءَامَنَ بِهِۦ وَتَبۡغُونَهَا عِوَجٗاۚ وَٱذۡكُرُوٓاْ إِذۡ كُنتُمۡ قَلِيلٗا فَكَثَّرَكُمۡۖ وَٱنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُفۡسِدِينَ

“Ndipo musamawakhalire anthu pa njira iliyonse mowabisalira ndi kumawaopseza, ndi kuwatsekereza kuyenda pa njira ya Allah amene amkhulupirira Iye, ndi kufuna kuikhotetsa njirayo (kuti anthu asaitsate). Ndipo kumbukirani pamene mudali ochepa nakuchulukitsani. Ndipo onani momwe adalili mapeto a owononga.” info
التفاسير:

external-link copy
87 : 7

وَإِن كَانَ طَآئِفَةٞ مِّنكُمۡ ءَامَنُواْ بِٱلَّذِيٓ أُرۡسِلۡتُ بِهِۦ وَطَآئِفَةٞ لَّمۡ يُؤۡمِنُواْ فَٱصۡبِرُواْ حَتَّىٰ يَحۡكُمَ ٱللَّهُ بَيۡنَنَاۚ وَهُوَ خَيۡرُ ٱلۡحَٰكِمِينَ

“Ndipo ngati pali gulu la anthu mwa inu amene akhulupirira uthenga umene ndatumidwa nawo, ndi gulu la anthu limene silidakhulupirire, pirirani mpaka Allah aweruze pakati pathu. Iye Ngwabwino poweruza kuposa oweruza.” info
التفاسير: