ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ

ಪುಟ ಸಂಖ್ಯೆ:close

external-link copy
9 : 62

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِذَا نُودِيَ لِلصَّلَوٰةِ مِن يَوۡمِ ٱلۡجُمُعَةِ فَٱسۡعَوۡاْ إِلَىٰ ذِكۡرِ ٱللَّهِ وَذَرُواْ ٱلۡبَيۡعَۚ ذَٰلِكُمۡ خَيۡرٞ لَّكُمۡ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ

E inu amene mwakhulupirira! Kukaitanidwa ku Swala (pemphero la Ijuma) tsiku la Ijuma, pitani mwachangu kukamtamanda Allah. Ndipo siyani malonda; zimenezo (mwalamulidwazo) nzabwino kwa inu ngati mukudziwa.[363] info

[363] M’ndime imeneyi akutiphunzitsa kuti tikamva adhana (kuitana) tsiku la Ijuma, tisiye chilichonse chimene tikuchita ndi kupita mwachangu kukapemphera pemphero la Ijuma. Pempheroli ndilofunika kwa msilamu aliyense makamaka amuna. Asilamu amasonkhana m’Misikiti ikuluikulu pa tsiku limeneli pa sabata iliyonse. Ndipo pa tsiku limeneli ndipomwe Allah adakwaniritsa zolenga zake zonse. Adam adalengedwa pa tsikuli ndipo adalowetsedwa ku Jannah tsiku lomweli. Ndipo adatulutsidwa m’menemo pa tsiku la Ijuma. Mtumiki adafotokozanso za kuti Qiyâma idzadza tsiku la Ijuma.

التفاسير:

external-link copy
10 : 62

فَإِذَا قُضِيَتِ ٱلصَّلَوٰةُ فَٱنتَشِرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَٱبۡتَغُواْ مِن فَضۡلِ ٱللَّهِ وَٱذۡكُرُواْ ٱللَّهَ كَثِيرٗا لَّعَلَّكُمۡ تُفۡلِحُونَ

Choncho Swala (ya Ijumayo) ikatha, balalikanani pa dziko, ndipo funani ubwino wa Allah; ndipo mtamandeni Allah kwambiri kuti mupambane (pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 62

وَإِذَا رَأَوۡاْ تِجَٰرَةً أَوۡ لَهۡوًا ٱنفَضُّوٓاْ إِلَيۡهَا وَتَرَكُوكَ قَآئِمٗاۚ قُلۡ مَا عِندَ ٱللَّهِ خَيۡرٞ مِّنَ ٱللَّهۡوِ وَمِنَ ٱلتِّجَٰرَةِۚ وَٱللَّهُ خَيۡرُ ٱلرَّٰزِقِينَ

Ndipo akaona malonda kapena masewero, akubalalika kunka ku zimenezo ndi kukusiya uli chiimire (ukuchita khutuba ndi anthu ochepa). Nena (kwa iwo): “Zimene zili kwa Allah nzabwino kwa inu kuposa masewero ndi malonda. Ndipo Allah Ngwabwino kwambiri kuposa opatsa onse.” info
التفاسير: