ಪವಿತ್ರ ಕುರ್‌ಆನ್ ಅರ್ಥಾನುವಾದ - ಚೇವಾ ಅನುವಾದ - ಖಾಲಿದ್ ಇಬ್ರಾಹೀಂ ಬೀತಾಲಾ

ಪುಟ ಸಂಖ್ಯೆ:close

external-link copy
45 : 53

وَأَنَّهُۥ خَلَقَ ٱلزَّوۡجَيۡنِ ٱلذَّكَرَ وَٱلۡأُنثَىٰ

Ndipo Iye ndiAmene adalenga mitundu iwiri: chachimuna ndi chachikazi, (anthu ndi zamoyo zina). info
التفاسير:

external-link copy
46 : 53

مِن نُّطۡفَةٍ إِذَا تُمۡنَىٰ

Kuchokera m’mbewu ya moyo pamene imafwamphukira (m’chiberekero). info
التفاسير:

external-link copy
47 : 53

وَأَنَّ عَلَيۡهِ ٱلنَّشۡأَةَ ٱلۡأُخۡرَىٰ

Ndipo ndithu ndi udindo Wake kuukitsa kwina (pambuyo pa imfa). info
التفاسير:

external-link copy
48 : 53

وَأَنَّهُۥ هُوَ أَغۡنَىٰ وَأَقۡنَىٰ

Ndipo Iye ndiAmene amapatsa chokwanira ndipo ndi amene amapatsa chosunga. info
التفاسير:

external-link copy
49 : 53

وَأَنَّهُۥ هُوَ رَبُّ ٱلشِّعۡرَىٰ

Ndipo ndithu Iye ndi Mbuye wa nyenyezi yotchedwa Shiira; info
التفاسير:

external-link copy
50 : 53

وَأَنَّهُۥٓ أَهۡلَكَ عَادًا ٱلۡأُولَىٰ

Ndipo Iye ndi amene adaononga Âdi oyamba; (anthu a Mneneri Hûd). info
التفاسير:

external-link copy
51 : 53

وَثَمُودَاْ فَمَآ أَبۡقَىٰ

Ndi Samudu; (anthu a Mneneri Swaleh;) choncho sadasiye (ndi mmodzi yemwe wa iwo). info
التفاسير:

external-link copy
52 : 53

وَقَوۡمَ نُوحٖ مِّن قَبۡلُۖ إِنَّهُمۡ كَانُواْ هُمۡ أَظۡلَمَ وَأَطۡغَىٰ

Ndipo (adawaononganso) anthu a Nuh, kale (asadaononge Âdi ndi Samudu). Ndithu iwo adali osalungama ndi olumpha malire kwambiri (kuposa Âdi ndi Samudu). info
التفاسير:

external-link copy
53 : 53

وَٱلۡمُؤۡتَفِكَةَ أَهۡوَىٰ

Ndi midzi yotembenuzidwa kumwamba kukhala pansi, pansi kukhala kumwamba, (ya anthu a Luti) adaigwetsa. info
التفاسير:

external-link copy
54 : 53

فَغَشَّىٰهَا مَا غَشَّىٰ

Tero chidaivindikira (midziyo) chomwe chidaivindikira (chilango). info
التفاسير:

external-link copy
55 : 53

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكَ تَتَمَارَىٰ

Kodi ndimtendere uti (mumtendere) wa Mbuye wako umene ukuukaikira? info
التفاسير:

external-link copy
56 : 53

هَٰذَا نَذِيرٞ مِّنَ ٱلنُّذُرِ ٱلۡأُولَىٰٓ

Uyu (Mtumiki) ndimchenjezi mwa achenjezi oyamba (amene adachenjezedwa nawo anthu a mibadwo yakale) info
التفاسير:

external-link copy
57 : 53

أَزِفَتِ ٱلۡأٓزِفَةُ

Chayandikira choyandikira (Qiyâma). info
التفاسير:

external-link copy
58 : 53

لَيۡسَ لَهَا مِن دُونِ ٱللَّهِ كَاشِفَةٌ

Palibe amene angachionetse koma Allah Yekha. info
التفاسير:

external-link copy
59 : 53

أَفَمِنۡ هَٰذَا ٱلۡحَدِيثِ تَعۡجَبُونَ

Kodi mukuidabwa nkhaniyi (ya Qur’an moikana)? info
التفاسير:

external-link copy
60 : 53

وَتَضۡحَكُونَ وَلَا تَبۡكُونَ

Mungoseka (mwachipongwe) ndipo simukulira (pamene mukuimva monga momwe akuchitira okhulupirira). info
التفاسير:

external-link copy
61 : 53

وَأَنتُمۡ سَٰمِدُونَ

Ndipo mukunyozera? info
التفاسير:

external-link copy
62 : 53

فَٱسۡجُدُواْۤ لِلَّهِۤ وَٱعۡبُدُواْ۩

Mlambireni ndi kumpembedza Allah (amene wavumbulutsa Qur’an kuti ikhale chiongoko cha anthu). info
التفاسير: