ការបកប្រែអត្ថន័យគួរអាន - ការបកប្រែជាភាសាឆេវ៉ា - ខលីទ អុីប្រហុីម ប៊ីតាឡា

លេខ​ទំព័រ:close

external-link copy
44 : 7

وَنَادَىٰٓ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَنَّةِ أَصۡحَٰبَ ٱلنَّارِ أَن قَدۡ وَجَدۡنَا مَا وَعَدَنَا رَبُّنَا حَقّٗا فَهَلۡ وَجَدتُّم مَّا وَعَدَ رَبُّكُمۡ حَقّٗاۖ قَالُواْ نَعَمۡۚ فَأَذَّنَ مُؤَذِّنُۢ بَيۡنَهُمۡ أَن لَّعۡنَةُ ٱللَّهِ عَلَى ٱلظَّٰلِمِينَ

Anthu a ku Munda wamtendere adzaitana anthu aku Moto (adzanena kuti): “Ndithudi ife tapeza zimene Mbuye wathu adatilonjeza kuti nzoona. Kodi nanunso mwapeza zomwe Mbuye wanu adakulonjezani kuti nzoona?” (Anthu a ku Moto) adzanena: “Inde.” Choncho wolengeza pakati pawo adzalengeza kuti: “Matembelero a Allah ali pa anthu ochita zoipa.” info
التفاسير:

external-link copy
45 : 7

ٱلَّذِينَ يَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ وَيَبۡغُونَهَا عِوَجٗا وَهُم بِٱلۡأٓخِرَةِ كَٰفِرُونَ

“Omwe ankaletsa anthu kuyenda pa njira ya Allah nafuna kuikhotetsa njirayo (kuti ioneke yokhota pamaso pa anthu), omwenso sadakhulupirire za tsiku lachimaliziro.” info
التفاسير:

external-link copy
46 : 7

وَبَيۡنَهُمَا حِجَابٞۚ وَعَلَى ٱلۡأَعۡرَافِ رِجَالٞ يَعۡرِفُونَ كُلَّۢا بِسِيمَىٰهُمۡۚ وَنَادَوۡاْ أَصۡحَٰبَ ٱلۡجَنَّةِ أَن سَلَٰمٌ عَلَيۡكُمۡۚ لَمۡ يَدۡخُلُوهَا وَهُمۡ يَطۡمَعُونَ

Ndipo pakati pawo (pa anthu a ku Munda wamtendere ndi a ku Moto) padzakhala chotchinga. Ndipo pamwamba pachikweza padzakhala anthu ena (ofanana ntchito zawo zabwino ndi zoyipa) omwe akazindikira onse (a ku Jannah ndi ku Moto), ndi zizindikiro zawo. Ndipo akawaitana anthu a ku Jannah (kuti): “Salaamun Alayikum (mtendere ukhale pa inu).” Koma asanailowe uku ali ndi chikhulupiliro (kuti ailowa). info
التفاسير:

external-link copy
47 : 7

۞ وَإِذَا صُرِفَتۡ أَبۡصَٰرُهُمۡ تِلۡقَآءَ أَصۡحَٰبِ ٱلنَّارِ قَالُواْ رَبَّنَا لَا تَجۡعَلۡنَا مَعَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ

Ndipo maso awo akakatembenuzidwa (kuyang’ana) ku mbali ya anthu a ku Moto, adzanena: “Mbuye wathu musatiike pamodzi ndi anthu ochita zoipa. (Tikhululukireni zolakwa zathu. Tilowetseni ku Jannah).” info
التفاسير:

external-link copy
48 : 7

وَنَادَىٰٓ أَصۡحَٰبُ ٱلۡأَعۡرَافِ رِجَالٗا يَعۡرِفُونَهُم بِسِيمَىٰهُمۡ قَالُواْ مَآ أَغۡنَىٰ عَنكُمۡ جَمۡعُكُمۡ وَمَا كُنتُمۡ تَسۡتَكۡبِرُونَ

Ndipo anthu aja apachikweza adzawaitana anthu (a ku Moto), adzawadziwa ndi zizindikiro zawo, nati: “Sikudakuthandizeni kuchuluka kwanu kuja, ngakhale zija mudali kudzitama nazo.” info
التفاسير:

external-link copy
49 : 7

أَهَٰٓؤُلَآءِ ٱلَّذِينَ أَقۡسَمۡتُمۡ لَا يَنَالُهُمُ ٱللَّهُ بِرَحۡمَةٍۚ ٱدۡخُلُواْ ٱلۡجَنَّةَ لَا خَوۡفٌ عَلَيۡكُمۡ وَلَآ أَنتُمۡ تَحۡزَنُونَ

“Kodi awa siaja munkawalumbilira kuti Allah sangawaninkhe chifundo? (Taonani tsopano, auzidwa kuti): “Lowani ku Jannah. Palibe mantha pa inu, ndiponso simudandaula.” info
التفاسير:

external-link copy
50 : 7

وَنَادَىٰٓ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِ أَصۡحَٰبَ ٱلۡجَنَّةِ أَنۡ أَفِيضُواْ عَلَيۡنَا مِنَ ٱلۡمَآءِ أَوۡ مِمَّا رَزَقَكُمُ ٱللَّهُۚ قَالُوٓاْ إِنَّ ٱللَّهَ حَرَّمَهُمَا عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ

Naonso anthu a ku Moto adzaitana a ku Jannah (ndikuwauza kuti): “Tatipungulirani madzi kapena chinthu chimene Allah wakupatsani.” (Anthu a ku Jannah) adzanena kuti:“Ndithu Allah waletsa kupereka zonse ziwirizo kwa osakhulupirira.” info
التفاسير:

external-link copy
51 : 7

ٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ دِينَهُمۡ لَهۡوٗا وَلَعِبٗا وَغَرَّتۡهُمُ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَاۚ فَٱلۡيَوۡمَ نَنسَىٰهُمۡ كَمَا نَسُواْ لِقَآءَ يَوۡمِهِمۡ هَٰذَا وَمَا كَانُواْ بِـَٔايَٰتِنَا يَجۡحَدُونَ

Omwe adachita chipembedzo chawo kukhala zinthu zopanda pake ndiponso masewero; ndipo udawanyenga moyo wa m’dziko. Choncho, lero Ifenso tiwaiwala (tiwaleka ku Moto) monga momwe adakuiwalira kukumana ndi tsiku lawo ili, ndi chifukwa chakukana kwawo zivumbulutso Zathu. info
التفاسير: