Terjemahan makna Alquran Alkarim - Terjemahan Berbahasa Chichewa - Khalid Ibrahim Betala

external-link copy
58 : 7

وَٱلۡبَلَدُ ٱلطَّيِّبُ يَخۡرُجُ نَبَاتُهُۥ بِإِذۡنِ رَبِّهِۦۖ وَٱلَّذِي خَبُثَ لَا يَخۡرُجُ إِلَّا نَكِدٗاۚ كَذَٰلِكَ نُصَرِّفُ ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمٖ يَشۡكُرُونَ

Ndipo m’nthaka yabwino umatuluka mmera wake (mwachangu) mwachilolezo cha Mbuye wake. Ndipo nthaka yomwe ili yoipa siitulutsa (mmera wake) koma movutikira. M’menemo ndi momwe Tikuchifotokozera chivumbulutso momveka kwa anthu oyamika.[186] info

[186] Mmene ilili nthaka yopanda chonde pomeretsa mmera movutikira nchimodzimodzi ndi anthu oipa. Nkovuta kuwaika pa njira yabwino. Koma tisatope ndi kutaya mtima nawo. Tiyesetsebe kuwakokera ku njira yabwino.

التفاسير: