Terjemahan makna Alquran Alkarim - Terjemahan Berbahasa Chichewa - Khalid Ibrahim Betala

external-link copy
187 : 7

يَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلسَّاعَةِ أَيَّانَ مُرۡسَىٰهَاۖ قُلۡ إِنَّمَا عِلۡمُهَا عِندَ رَبِّيۖ لَا يُجَلِّيهَا لِوَقۡتِهَآ إِلَّا هُوَۚ ثَقُلَتۡ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ لَا تَأۡتِيكُمۡ إِلَّا بَغۡتَةٗۗ يَسۡـَٔلُونَكَ كَأَنَّكَ حَفِيٌّ عَنۡهَاۖ قُلۡ إِنَّمَا عِلۡمُهَا عِندَ ٱللَّهِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ

Akukufunsa za nthawi (ya Qiyâma) kuti idzakhalako liti? Nena: “Kudziwika kwa nthawi yake kuli kwa Mbuye wanga. palibe amene angaionetse poyera nthawi yake koma Iye. Nkovuta kwambiri kumwamba ndi pansi (kuizindikira nthawi yake). Siidzakudzerani koma mwadzidzidzi.” Akukufunsa ngati kuti iwe ukudziwa bwino za nthawiyo. Nena: “Kudziwika kwa nthawi yake kuli kwa Allah. Koma anthu ambiri sadziwa.” info
التفاسير: