Terjemahan makna Alquran Alkarim - Terjemahan Berbahasa Chichewa - Khalid Ibrahim Betala

At-Tûr

external-link copy
1 : 52

وَٱلطُّورِ

Ndikulumbilira phiri la Turi (ku Sinai pamene Mûsa adalankhulana ndi Allah). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 52

وَكِتَٰبٖ مَّسۡطُورٖ

Ndi buku lolembedwa. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 52

فِي رَقّٖ مَّنشُورٖ

M’mipukutu yazikopa zotambasuka (zosavuta kuwerenga). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 52

وَٱلۡبَيۡتِ ٱلۡمَعۡمُورِ

Ndi nyumba yopitako kawirikawiri (pochitamo mapemphero). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 52

وَٱلسَّقۡفِ ٱلۡمَرۡفُوعِ

Ndi thambo limene latukulidwa (popanda mzati). info
التفاسير:

external-link copy
6 : 52

وَٱلۡبَحۡرِ ٱلۡمَسۡجُورِ

Ndi nyanja yodzadza ndi madzi. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 52

إِنَّ عَذَابَ رَبِّكَ لَوَٰقِعٞ

Ndithu chilango cha Mbuye wako (chimene wawalonjeza nacho osakhulupirira) chiwapeza (popanda chipeneko). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 52

مَّا لَهُۥ مِن دَافِعٖ

Palibe wochichotsa (pa iwo). info
التفاسير:

external-link copy
9 : 52

يَوۡمَ تَمُورُ ٱلسَّمَآءُ مَوۡرٗا

Pa tsikulo thambo lidzagwedezeka; kugwedezeka kwamphamvu. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 52

وَتَسِيرُ ٱلۡجِبَالُ سَيۡرٗا

Ndipo mapiri adzayenda mwamphavu (kuchoka m’malo mwake). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 52

فَوَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Kuonongeka koopsa pa tsiku limenelo kuzakhala pa otsutsa choonadi. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 52

ٱلَّذِينَ هُمۡ فِي خَوۡضٖ يَلۡعَبُونَ

Iwo amene akungosewera mzinthu zopanda pake. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 52

يَوۡمَ يُدَعُّونَ إِلَىٰ نَارِ جَهَنَّمَ دَعًّا

Tsiku limene adzakankhidwira mwamphamvu ku Jahannam (ku Moto Woopsa). info
التفاسير:

external-link copy
14 : 52

هَٰذِهِ ٱلنَّارُ ٱلَّتِي كُنتُم بِهَا تُكَذِّبُونَ

(Kudzanenedwa kwa iwo): “Uwu ndi Moto uja umene mudali kuutsutsa (pa dziko lapansi) info
التفاسير: