Terjemahan makna Alquran Alkarim - Terjemahan Berbahasa Chichewa - Khalid Ibrahim Betala

external-link copy
37 : 12

قَالَ لَا يَأۡتِيكُمَا طَعَامٞ تُرۡزَقَانِهِۦٓ إِلَّا نَبَّأۡتُكُمَا بِتَأۡوِيلِهِۦ قَبۡلَ أَن يَأۡتِيَكُمَاۚ ذَٰلِكُمَا مِمَّا عَلَّمَنِي رَبِّيٓۚ إِنِّي تَرَكۡتُ مِلَّةَ قَوۡمٖ لَّا يُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَهُم بِٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ كَٰفِرُونَ

(Yûsuf) adati: “(Kupyolera mu uneneri umene ndapatsidwa ndingathe kukumasulirani maloto anuwa ndi zinthu zina zobisika kwa inu), sichikudzerani chakudya cha mtundu uliwonse choti mungapatsidwe koma ndikhala nditakumasulirani tanthauzo lake chisanakufikeni; (ngati mukufunadi ndikuchitirani zimenezi). Izi ndi zina mwa zomwe Mbuye wanga wandiphunzitsa. Ndithudi, ine ndasiya njira za anthu osakhulupirira Allah ndiponso omwe akukana za tsiku la chimaliziro.” info
التفاسير: