क़ुरआन के अर्थों का अनुवाद - चेवा अनुवाद - ख़ालिद अबराहीम बेताला

Al-Jinn

external-link copy
1 : 72

قُلۡ أُوحِيَ إِلَيَّ أَنَّهُ ٱسۡتَمَعَ نَفَرٞ مِّنَ ٱلۡجِنِّ فَقَالُوٓاْ إِنَّا سَمِعۡنَا قُرۡءَانًا عَجَبٗا

Nena (iwe Mtumiki (s.a.w), kwa anthu ako): “Kwavumbulutsidwa kwa ine kuti gulu la ziwanda lidamvetsera (kuwerenga kwanga kwa Qur’an) ndipo lidanena (kumtundu wawo): ndithu tamvetsera Qur’an yodabwitsa (ikuwerengedwa). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 72

يَهۡدِيٓ إِلَى ٱلرُّشۡدِ فَـَٔامَنَّا بِهِۦۖ وَلَن نُّشۡرِكَ بِرَبِّنَآ أَحَدٗا

Ikuitanira kuchilungamo, ndipo taikhulupirira. Ndipo sitimphatikiza aliyense ndi Mbuye wathu, (pa mapemphero). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 72

وَأَنَّهُۥ تَعَٰلَىٰ جَدُّ رَبِّنَا مَا ٱتَّخَذَ صَٰحِبَةٗ وَلَا وَلَدٗا

Ndipo ndithu ukulu ndi ulemelero wa Mbuye wathu watukuka; sadadzipangire mkazi kapena mwana. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 72

وَأَنَّهُۥ كَانَ يَقُولُ سَفِيهُنَا عَلَى ٱللَّهِ شَطَطٗا

Ndipo ndithu mbuli za mwa ife zakhala zikunenera Allah mawu abodza (okhala kutali ndi choonadi). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 72

وَأَنَّا ظَنَنَّآ أَن لَّن تَقُولَ ٱلۡإِنسُ وَٱلۡجِنُّ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبٗا

Ndipo ndithu ife tinkaganiza kuti anthu ndi ziwanda sangamnenere Allah zabodza (zosayenera ulemelero Wake). info
التفاسير:

external-link copy
6 : 72

وَأَنَّهُۥ كَانَ رِجَالٞ مِّنَ ٱلۡإِنسِ يَعُوذُونَ بِرِجَالٖ مِّنَ ٱلۡجِنِّ فَزَادُوهُمۡ رَهَقٗا

Ndipo ndithu padali amuna a mu wanthu amapempha chitetezo kwa amuna amziwanda, ndipo adawaonjezera (amuna amziwanda) kupitiriza machimo (awo, kupulikira ndi kuchenjelera anthu). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 72

وَأَنَّهُمۡ ظَنُّواْ كَمَا ظَنَنتُمۡ أَن لَّن يَبۡعَثَ ٱللَّهُ أَحَدٗا

Ndipo ndithu iwo amaganiza monga momwe mumaganizira inu kuti Allah sadzaukitsa aliyense. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 72

وَأَنَّا لَمَسۡنَا ٱلسَّمَآءَ فَوَجَدۡنَٰهَا مُلِئَتۡ حَرَسٗا شَدِيدٗا وَشُهُبٗا

Ndithu ife tidafuna kukafika kumwamba; tidakupeza kutadzala alonda (angelo) amphamvu ndi zenje za moto. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 72

وَأَنَّا كُنَّا نَقۡعُدُ مِنۡهَا مَقَٰعِدَ لِلسَّمۡعِۖ فَمَن يَسۡتَمِعِ ٱلۡأٓنَ يَجِدۡ لَهُۥ شِهَابٗا رَّصَدٗا

Ndithu ife tidali kukhala m’menemo (kale) mokhala momvetsera; (mobera nkhani zakumwamba). Koma amene afune kumvetsera tsopano apeza chenje cha moto chikudikilira (kuti chimgwere iye ndi kumuononga). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 72

وَأَنَّا لَا نَدۡرِيٓ أَشَرٌّ أُرِيدَ بِمَن فِي ٱلۡأَرۡضِ أَمۡ أَرَادَ بِهِمۡ رَبُّهُمۡ رَشَدٗا

Ndithu ife sitikudziwa chilango chimene akuwafunira a m’dziko (polondera kumwamba, kuletsa kumvetsera nkhani zakumeneko); kapena Mbuye wawo akuwafunira zabwino ndi chilungamo (pa zimenezo)! info
التفاسير:

external-link copy
11 : 72

وَأَنَّا مِنَّا ٱلصَّٰلِحُونَ وَمِنَّا دُونَ ذَٰلِكَۖ كُنَّا طَرَآئِقَ قِدَدٗا

Ndithu ena mwa ife ndi abwino koma ena sali choncho. Tili njira zosiyanasiyana. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 72

وَأَنَّا ظَنَنَّآ أَن لَّن نُّعۡجِزَ ٱللَّهَ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَن نُّعۡجِزَهُۥ هَرَبٗا

Ndithu ife tidadziwa kuti Allah sitingathe kumlepheretsa (lamulo Lake pa ife paliponse tingakhale) pa dziko lapansi, ndipo sitingamlepheretsenso pomzemba ndi kuthawira (kumwamba). info
التفاسير:

external-link copy
13 : 72

وَأَنَّا لَمَّا سَمِعۡنَا ٱلۡهُدَىٰٓ ءَامَنَّا بِهِۦۖ فَمَن يُؤۡمِنۢ بِرَبِّهِۦ فَلَا يَخَافُ بَخۡسٗا وَلَا رَهَقٗا

Ndipo ife pamene tachimva chiongoko (Qur’an) tachikhulupirira ndipo amene ati akhulupirire mwa Mbuye wake saopa kumchepetsera (chabwino kapena kumuonjezera machimo ake). info
التفاسير: