क़ुरआन के अर्थों का अनुवाद - चेवा अनुवाद - ख़ालिद अबराहीम बेताला

पृष्ठ संख्या:close

external-link copy
26 : 40

وَقَالَ فِرۡعَوۡنُ ذَرُونِيٓ أَقۡتُلۡ مُوسَىٰ وَلۡيَدۡعُ رَبَّهُۥٓۖ إِنِّيٓ أَخَافُ أَن يُبَدِّلَ دِينَكُمۡ أَوۡ أَن يُظۡهِرَ فِي ٱلۡأَرۡضِ ٱلۡفَسَادَ

Ndipo Farawo adati: “Ndilekeni ndimuphe Mûsa; ampemphe Mbuye wakeyo (kuti ampulumutse kwa ine). Ine ndikuopera kuti angasinthe chipembedzo chanu, kapena kufalitsa chisokonezo pa dziko.” info
التفاسير:

external-link copy
27 : 40

وَقَالَ مُوسَىٰٓ إِنِّي عُذۡتُ بِرَبِّي وَرَبِّكُم مِّن كُلِّ مُتَكَبِّرٖ لَّا يُؤۡمِنُ بِيَوۡمِ ٱلۡحِسَابِ

Ndipo Mûsa adati (kwa Farawo pa modzi ndi anthu ake): “Ine ndadzitchinjiriza ndi Mbuye wanga amenenso ali Mbuye wanu (ku chiwembu) chochokera kwa aliyense wodzikweza, wosakhulupirira za tsiku la chiwerengero. info
التفاسير:

external-link copy
28 : 40

وَقَالَ رَجُلٞ مُّؤۡمِنٞ مِّنۡ ءَالِ فِرۡعَوۡنَ يَكۡتُمُ إِيمَٰنَهُۥٓ أَتَقۡتُلُونَ رَجُلًا أَن يَقُولَ رَبِّيَ ٱللَّهُ وَقَدۡ جَآءَكُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ مِن رَّبِّكُمۡۖ وَإِن يَكُ كَٰذِبٗا فَعَلَيۡهِ كَذِبُهُۥۖ وَإِن يَكُ صَادِقٗا يُصِبۡكُم بَعۡضُ ٱلَّذِي يَعِدُكُمۡۖ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي مَنۡ هُوَ مُسۡرِفٞ كَذَّابٞ

Ndipo munthu wokhulupirira, wochokera kubanja la Farawo yemwe adali kubisa chikhulupiliro chake, adawalankhula (anthu ake): “Kodi muphe munthu chifukwa chakuti iye akunena kuti: ‘Mbuye wanga ndi Allah,’ chikhalirecho wakubweretserani zisonyezo zoonekera poyera, zochokera kwa Mbuye wanu? Ndipo ngati ali wabodza pa zomwe akunena ndiye kuti kuipa kwa bodzalo kum’bwerera yekha. Koma ngati ali woona (pazomwe akukulonjezani), ndiye kuti gawo lina la zomwe (chilango) akukulonjezani likupezani; ndithu Allah saongola munthu wopyola malire, wabodza la mkunkhuniza!” info
التفاسير:

external-link copy
29 : 40

يَٰقَوۡمِ لَكُمُ ٱلۡمُلۡكُ ٱلۡيَوۡمَ ظَٰهِرِينَ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَمَن يَنصُرُنَا مِنۢ بَأۡسِ ٱللَّهِ إِن جَآءَنَاۚ قَالَ فِرۡعَوۡنُ مَآ أُرِيكُمۡ إِلَّا مَآ أَرَىٰ وَمَآ أَهۡدِيكُمۡ إِلَّا سَبِيلَ ٱلرَّشَادِ

“E inu anthu anga! Ufumu walero ngwanu: mwagonjetsa dziko (la Iguputo). Ndani amene angatipulumutse ku chilango cha Allah ngati chitatidzera?” Farawo adati: “Sindikukupatsani maganizo koma okhawo ndikuwaona (kuti ndi abwino) ndiponso sindikukuwongolerani koma kunjira yoongoka.” info
التفاسير:

external-link copy
30 : 40

وَقَالَ ٱلَّذِيٓ ءَامَنَ يَٰقَوۡمِ إِنِّيٓ أَخَافُ عَلَيۡكُم مِّثۡلَ يَوۡمِ ٱلۡأَحۡزَابِ

Ndipo munthu wokhulupirira uja adanena: “E inu anthu anga! Ine ndikukuoperani (za tsiku la masautso) monga tsiku la magulu (omwe adaukira aneneri awo).” info
التفاسير:

external-link copy
31 : 40

مِثۡلَ دَأۡبِ قَوۡمِ نُوحٖ وَعَادٖ وَثَمُودَ وَٱلَّذِينَ مِنۢ بَعۡدِهِمۡۚ وَمَا ٱللَّهُ يُرِيدُ ظُلۡمٗا لِّلۡعِبَادِ

“Monga chikhalidwe cha anthu a Nuh, Âdi, Samudi ndi anthu omwe adadza pambuyo pawo. Koma Allah safuna kupondereza akapolo Ake.” info
التفاسير:

external-link copy
32 : 40

وَيَٰقَوۡمِ إِنِّيٓ أَخَافُ عَلَيۡكُمۡ يَوۡمَ ٱلتَّنَادِ

“Ndiponso anthu anga! Ine ndikukuoperani tsiku la kuitanizana (anthu).” info
التفاسير:

external-link copy
33 : 40

يَوۡمَ تُوَلُّونَ مُدۡبِرِينَ مَا لَكُم مِّنَ ٱللَّهِ مِنۡ عَاصِمٖۗ وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِنۡ هَادٖ

“Tsiku limene mudzathawa ndi kutembenuza misana yanu; pomwe simudzakhala ndi mtetezi ku chilango cha Allah; ndipo amene Allah wamulekelera kusokera (chifukwa cha zochita zake zoipa), ndiye kuti sangapeze muongoli.” info
التفاسير: