क़ुरआन के अर्थों का अनुवाद - चेवा अनुवाद - ख़ालिद अबराहीम बेताला

पृष्ठ संख्या:close

external-link copy
32 : 39

۞ فَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّن كَذَبَ عَلَى ٱللَّهِ وَكَذَّبَ بِٱلصِّدۡقِ إِذۡ جَآءَهُۥٓۚ أَلَيۡسَ فِي جَهَنَّمَ مَثۡوٗى لِّلۡكَٰفِرِينَ

۞ Kodi ndiyani wachinyengo wamkulu woposa yemwe akumnamizira Allah zabodza, ndi kutsutsa choona chikamdzera? Kodi Jahannam simalo a okanira? info
التفاسير:

external-link copy
33 : 39

وَٱلَّذِي جَآءَ بِٱلصِّدۡقِ وَصَدَّقَ بِهِۦٓ أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُتَّقُونَ

Ndipo amene wadza ndi choona, naachikhulupirira, iwowo ndiwo oopa Allah. info
التفاسير:

external-link copy
34 : 39

لَهُم مَّا يَشَآءُونَ عِندَ رَبِّهِمۡۚ ذَٰلِكَ جَزَآءُ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Adzapeza zomwe adzakhumba kwa Mbuye wawo. Imeneyo ndiyo mphoto ya ochita zabwino. info
التفاسير:

external-link copy
35 : 39

لِيُكَفِّرَ ٱللَّهُ عَنۡهُمۡ أَسۡوَأَ ٱلَّذِي عَمِلُواْ وَيَجۡزِيَهُمۡ أَجۡرَهُم بِأَحۡسَنِ ٱلَّذِي كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Kuti Allah awafafanizire zoipa za zochita zawo, ndi kuti awalipire malipiro awo chifukwa cha zabwino zomwe adali kuchita. info
التفاسير:

external-link copy
36 : 39

أَلَيۡسَ ٱللَّهُ بِكَافٍ عَبۡدَهُۥۖ وَيُخَوِّفُونَكَ بِٱلَّذِينَ مِن دُونِهِۦۚ وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِنۡ هَادٖ

Kodi Allah sali Wokwanira kwa kapolo Wake? Koma akukuopseza ndi zina zosakhala Iye! Ndipo yemwe Allah wam’lekelera kuti asokere, ndithu alibe womuongola. info
التفاسير:

external-link copy
37 : 39

وَمَن يَهۡدِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِن مُّضِلٍّۗ أَلَيۡسَ ٱللَّهُ بِعَزِيزٖ ذِي ٱنتِقَامٖ

Ndipo amene Allah wamuongola, palibe amene angathe kumsokeretsa. Kodi Allah sali Mwini mphamvu zoposa; Wokhoza kubwezera chilango? info
التفاسير:

external-link copy
38 : 39

وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّنۡ خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ لَيَقُولُنَّ ٱللَّهُۚ قُلۡ أَفَرَءَيۡتُم مَّا تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ إِنۡ أَرَادَنِيَ ٱللَّهُ بِضُرٍّ هَلۡ هُنَّ كَٰشِفَٰتُ ضُرِّهِۦٓ أَوۡ أَرَادَنِي بِرَحۡمَةٍ هَلۡ هُنَّ مُمۡسِكَٰتُ رَحۡمَتِهِۦۚ قُلۡ حَسۡبِيَ ٱللَّهُۖ عَلَيۡهِ يَتَوَكَّلُ ٱلۡمُتَوَكِّلُونَ

Ndipo ukawafunsa (kuti) ndani adalenga thambo ndi nthaka, ndithu anena (kuti ndi) “Allah.” Nena: “Kodi mukuona bwanji, amene mukuwapembedza kusiya Allah angandichotsere masautso ake ngati Allah atafuna kundipatsa masautso? Kapena Allah atafuna kundichitira chifundo, kodi iwo angatsekereze chifundo Chakecho?” Nena: “Allah akundikwanira! Kwa Iye, atsamire otsamira.” info
التفاسير:

external-link copy
39 : 39

قُلۡ يَٰقَوۡمِ ٱعۡمَلُواْ عَلَىٰ مَكَانَتِكُمۡ إِنِّي عَٰمِلٞۖ فَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ

Nena: “E inu anthu anga! Chitani zochita zanu mmene mungathere. Nanenso ndichita (mmene ndingathere). Koma posachedwa mudziwa. info
التفاسير:

external-link copy
40 : 39

مَن يَأۡتِيهِ عَذَابٞ يُخۡزِيهِ وَيَحِلُّ عَلَيۡهِ عَذَابٞ مُّقِيمٌ

Amene chim’dzere chilango chomuyalutsa, ndi kum’fikira iye chilango chamuyaya.” info
التفاسير: