क़ुरआन के अर्थों का अनुवाद - चेवा अनुवाद - ख़ालिद अबराहीम बेताला

पृष्ठ संख्या:close

external-link copy
44 : 28

وَمَا كُنتَ بِجَانِبِ ٱلۡغَرۡبِيِّ إِذۡ قَضَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَى ٱلۡأَمۡرَ وَمَا كُنتَ مِنَ ٱلشَّٰهِدِينَ

Ndipo iwe sudali mbali ya kuzambwe (kwa phiri limenelo) pamene tidampatsa Mûsa lamulo; sudalinso mwa amene adalipo (pamalopo). info
التفاسير:

external-link copy
45 : 28

وَلَٰكِنَّآ أَنشَأۡنَا قُرُونٗا فَتَطَاوَلَ عَلَيۡهِمُ ٱلۡعُمُرُۚ وَمَا كُنتَ ثَاوِيٗا فِيٓ أَهۡلِ مَدۡيَنَ تَتۡلُواْ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتِنَا وَلَٰكِنَّا كُنَّا مُرۡسِلِينَ

Koma ife tidaumba mibadwo yambiri (pambuyo pa Mneneri Mûsa) kotero kuti zaka zidapitapo zambiri pakati pawo. Ndipo sudakhale nawo anthu a Madiyan ndi kumawawerengera Ayah (ndime) Zathu; koma Ife tidali kutuma (atumiki ndi kuwafotokozera zomwe zidachitika patsogolo ndi pambuyo pawo, monga momwe takutumira iwe ndi kukudziwitsa nkhani zakale ndi zimene zikudza pambuyo). info
التفاسير:

external-link copy
46 : 28

وَمَا كُنتَ بِجَانِبِ ٱلطُّورِ إِذۡ نَادَيۡنَا وَلَٰكِن رَّحۡمَةٗ مِّن رَّبِّكَ لِتُنذِرَ قَوۡمٗا مَّآ أَتَىٰهُم مِّن نَّذِيرٖ مِّن قَبۡلِكَ لَعَلَّهُمۡ يَتَذَكَّرُونَ

Ndipo sudali kumbali kwa phiri pamene tidamuitana (Mneneri Mûsa). Koma (kutumidwa kwako) ndimtendere wochokera kwa Mbuye wako kuti uwachenjeze anthu omwe mchenjezi sadawadzere (mnthawi yaitali) iwe usadadze, kuti akumbukire. info
التفاسير:

external-link copy
47 : 28

وَلَوۡلَآ أَن تُصِيبَهُم مُّصِيبَةُۢ بِمَا قَدَّمَتۡ أَيۡدِيهِمۡ فَيَقُولُواْ رَبَّنَا لَوۡلَآ أَرۡسَلۡتَ إِلَيۡنَا رَسُولٗا فَنَتَّبِعَ ءَايَٰتِكَ وَنَكُونَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

(Ndipo sitikadatuma) koma kuti mavuto akawapeza ochokera (ku zoipa) zomwe atsogoza manja awo, amanena: “Mbuye wathu! Bwanji wosatitumizira Mtumiki kuti titsate mawu anu ndi kukhala mwa okhulupirira.” info
التفاسير:

external-link copy
48 : 28

فَلَمَّا جَآءَهُمُ ٱلۡحَقُّ مِنۡ عِندِنَا قَالُواْ لَوۡلَآ أُوتِيَ مِثۡلَ مَآ أُوتِيَ مُوسَىٰٓۚ أَوَلَمۡ يَكۡفُرُواْ بِمَآ أُوتِيَ مُوسَىٰ مِن قَبۡلُۖ قَالُواْ سِحۡرَانِ تَظَٰهَرَا وَقَالُوٓاْ إِنَّا بِكُلّٖ كَٰفِرُونَ

Koma choona pamene chidawadzera kuchokera kwa Ife, adati: “Bwanji sadapatsidwe zonga zomwe adapatsidwa Mûsa? (Monga kutembenuza ndodo kukhala njoka, ndi zina zotero).” Kodi kalelo sadazikane zomwe adapatsidwa Mûsa? Nkunena (za Taurati ndi Qur’an): “Ndimatsenga awiri amene akuthandizana.” Ndipo adati: “Ndithu ife tikuwakana onse.” info
التفاسير:

external-link copy
49 : 28

قُلۡ فَأۡتُواْ بِكِتَٰبٖ مِّنۡ عِندِ ٱللَّهِ هُوَ أَهۡدَىٰ مِنۡهُمَآ أَتَّبِعۡهُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ

Nena: “Bwerani nalo buku lochokera kwa Allah lomwe lili ndi chiongoko chabwino kuposa awiriwa (Taurati ya Mneneri Mûsa, ndi iyi Qur’an), kuti ndilitsate ngati inu mukunena zoona.” info
التفاسير:

external-link copy
50 : 28

فَإِن لَّمۡ يَسۡتَجِيبُواْ لَكَ فَٱعۡلَمۡ أَنَّمَا يَتَّبِعُونَ أَهۡوَآءَهُمۡۚ وَمَنۡ أَضَلُّ مِمَّنِ ٱتَّبَعَ هَوَىٰهُ بِغَيۡرِ هُدٗى مِّنَ ٱللَّهِۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلظَّٰلِمِينَ

Koma ngati sadakuyankhe, dziwa kuti akutsatira zilakolako zawo. Kodi ndani wasokera kwambiri kuposa yemwe akutsatira zilakolako zake popanda chiongoko chochokera kwa Allah? Ndithu Allah saongola anthu odzichitira zoipa. info
التفاسير: