કુરઆન મજીદના શબ્દોનું ભાષાંતર - ચિચેવા ભાષામાં અનુવાદ - ખાલિદ ઇબ્રાહિમ બૈતાલા

પેજ નંબર: 164:151 close

external-link copy
121 : 7

قَالُوٓاْ ءَامَنَّا بِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Adati: “Takhulupirira Mbuye wa zolengedwa zonse.” info
التفاسير:

external-link copy
122 : 7

رَبِّ مُوسَىٰ وَهَٰرُونَ

“Mbuye wa Mûsa Ndi Harun.” info
التفاسير:

external-link copy
123 : 7

قَالَ فِرۡعَوۡنُ ءَامَنتُم بِهِۦ قَبۡلَ أَنۡ ءَاذَنَ لَكُمۡۖ إِنَّ هَٰذَا لَمَكۡرٞ مَّكَرۡتُمُوهُ فِي ٱلۡمَدِينَةِ لِتُخۡرِجُواْ مِنۡهَآ أَهۡلَهَاۖ فَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ

Farawo adati: “Mwamkhulupirira chotani iye ndisanakupatseni chilolezo? Ndithu iyi ndi ndale yomwe mwaichita mu mzindamu (inu ndi Mûsa) kuti muwatulutsemo eni mzindawo. Koma posachedwa mudziwa (chimene ndikuchiteni).” info
التفاسير:

external-link copy
124 : 7

لَأُقَطِّعَنَّ أَيۡدِيَكُمۡ وَأَرۡجُلَكُم مِّنۡ خِلَٰفٖ ثُمَّ لَأُصَلِّبَنَّكُمۡ أَجۡمَعِينَ

“Ndithudi, nditseteka manja anu ndi miyendo yanu mosinthanitsa; (kudula dzanja lakudzanjadzanja ndi mwendo wa kumanzere, kapena dzanja la kumanzere ndi mwendo wakudzanjadzanja). Kenako ndikupachikani nonsenu.” info
التفاسير:

external-link copy
125 : 7

قَالُوٓاْ إِنَّآ إِلَىٰ رَبِّنَا مُنقَلِبُونَ

(Iwo) adati: “Ndithu ife kwa Mbuye wathu ngobwerera.” info
التفاسير:

external-link copy
126 : 7

وَمَا تَنقِمُ مِنَّآ إِلَّآ أَنۡ ءَامَنَّا بِـَٔايَٰتِ رَبِّنَا لَمَّا جَآءَتۡنَاۚ رَبَّنَآ أَفۡرِغۡ عَلَيۡنَا صَبۡرٗا وَتَوَفَّنَا مُسۡلِمِينَ

“Komatu palibe choipa chimene waona mwa ife kupatula kuti takhulupirira zizindikiro za Mbuye wathu pamene zatidzera. E Mbuye wathu! Titsanulireni chipiliro, ndipo tipatseni imfa uku tili Asilamu (ogonjera Inu).” info
التفاسير:

external-link copy
127 : 7

وَقَالَ ٱلۡمَلَأُ مِن قَوۡمِ فِرۡعَوۡنَ أَتَذَرُ مُوسَىٰ وَقَوۡمَهُۥ لِيُفۡسِدُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَيَذَرَكَ وَءَالِهَتَكَۚ قَالَ سَنُقَتِّلُ أَبۡنَآءَهُمۡ وَنَسۡتَحۡيِۦ نِسَآءَهُمۡ وَإِنَّا فَوۡقَهُمۡ قَٰهِرُونَ

Ndipo nduna za mwa anthu a Farawo zidati (kwa Farawo): “Kodi umuleka Mûsa ndi anthu ake kuti abwere ndi chisokonezo m’dziko, ndi kuti akusiye iwe ndi milungu yako (yomwe adatilangiza makolo athu kuti tipembedze pamodzi ndi iwe)? (Farawo) Adati: “Tipha ana awo achimuna ndikuwasiya amoyo (ana awo) achikazi. Ndithudi ife pa iwo tili ndi mphamvu zowagonjetsera.” info
التفاسير:

external-link copy
128 : 7

قَالَ مُوسَىٰ لِقَوۡمِهِ ٱسۡتَعِينُواْ بِٱللَّهِ وَٱصۡبِرُوٓاْۖ إِنَّ ٱلۡأَرۡضَ لِلَّهِ يُورِثُهَا مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦۖ وَٱلۡعَٰقِبَةُ لِلۡمُتَّقِينَ

Mûsa adauza anthu ake: “Pemphani chithandizo kwa Allah, ndipo pirirani. Ndithu dzikoli ndi la Allah; amalipereka kwa amene wamfuna mwa akapolo Ake. Ndipo mapeto abwino nga anthu olungama.” info
التفاسير:

external-link copy
129 : 7

قَالُوٓاْ أُوذِينَا مِن قَبۡلِ أَن تَأۡتِيَنَا وَمِنۢ بَعۡدِ مَا جِئۡتَنَاۚ قَالَ عَسَىٰ رَبُّكُمۡ أَن يُهۡلِكَ عَدُوَّكُمۡ وَيَسۡتَخۡلِفَكُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَيَنظُرَ كَيۡفَ تَعۡمَلُونَ

(Iwo) adati: “Takhala tikuzunzidwa usanatidzere ndiponso (tsopano) pamene watidzera.” (Mûsa) adati: “Mwina Mbuye wanu amuononga mdani wanu ndipo akuchitani kukhala alowammalo m’dzikoli, ndi kuti aone mmene mungachitire.” info
التفاسير:

external-link copy
130 : 7

وَلَقَدۡ أَخَذۡنَآ ءَالَ فِرۡعَوۡنَ بِٱلسِّنِينَ وَنَقۡصٖ مِّنَ ٱلثَّمَرَٰتِ لَعَلَّهُمۡ يَذَّكَّرُونَ

Ndithu tidawakhaulitsa anthu a Farawo ndi chilala, ndi kuchepekedwa zokolola; kuti mwina angakumbukire. info
التفاسير: