કુરઆન મજીદના શબ્દોનું ભાષાંતર - ચિચેવા ભાષામાં અનુવાદ - ખાલિદ ઇબ્રાહિમ બૈતાલા

Al-Mumtahnah

external-link copy
1 : 60

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَتَّخِذُواْ عَدُوِّي وَعَدُوَّكُمۡ أَوۡلِيَآءَ تُلۡقُونَ إِلَيۡهِم بِٱلۡمَوَدَّةِ وَقَدۡ كَفَرُواْ بِمَا جَآءَكُم مِّنَ ٱلۡحَقِّ يُخۡرِجُونَ ٱلرَّسُولَ وَإِيَّاكُمۡ أَن تُؤۡمِنُواْ بِٱللَّهِ رَبِّكُمۡ إِن كُنتُمۡ خَرَجۡتُمۡ جِهَٰدٗا فِي سَبِيلِي وَٱبۡتِغَآءَ مَرۡضَاتِيۚ تُسِرُّونَ إِلَيۡهِم بِٱلۡمَوَدَّةِ وَأَنَا۠ أَعۡلَمُ بِمَآ أَخۡفَيۡتُمۡ وَمَآ أَعۡلَنتُمۡۚ وَمَن يَفۡعَلۡهُ مِنكُمۡ فَقَدۡ ضَلَّ سَوَآءَ ٱلسَّبِيلِ

E inu amene mwakhulupirira! Musawachite adani Anga ndi adani anu kukhala athandizi anu ndi kumawauza (nkhani zanu) mwa chikondi, pomwe iwo sanakhulupirire choonadi chimene chakudzerani. Adamtulutsa Mtumiki ndi inu nomwe (m’nyumba zanu) chifukwa chakuti mumakhulupirira Allah, Mbuye wanu, (palibe cholakwa chilichonse chimene mudawachitira,) ngati mwatuluka kukachita Jihâd pa njira Yanga ndi kufunafuna chikondi Changa (musapalane nawo ubwenzi). Mukuwatumizira chinsinsi (chanu cha nkhondo) chifukwa cha chikondi (chanu ndi iwo); (musachitenso zimenezi) pomwe Ine ndikudziwa zimene inu mukubisa ndi zimenene mukuzisonyeza (poyera); amene akuchita zimenezi mwa inu, ndiye kuti wataya njira yoongoka.[355] info

[355] Inu Asilamu amene mwakhulupilira mwa Allah ndi Mthenga Wake (s.a.w) musawachite makafiri amene ndi adani anga ndiponso adani anu kukhala okondedwa anu ndi abwenzi anu. Chisonyezo cha chikhulupiliro kwa Msilamu ndiko kuwada adani a Allah, osati kuwakonda ndi kupalana nawo ubwenzi.

التفاسير:

external-link copy
2 : 60

إِن يَثۡقَفُوكُمۡ يَكُونُواْ لَكُمۡ أَعۡدَآءٗ وَيَبۡسُطُوٓاْ إِلَيۡكُمۡ أَيۡدِيَهُمۡ وَأَلۡسِنَتَهُم بِٱلسُّوٓءِ وَوَدُّواْ لَوۡ تَكۡفُرُونَ

Akakumana nanu (pankhondo) akukhala adani anu ndipo akukutambasulirani manja ndi malirime awo moipa (pokumenyani ndi kukutukwanani); ndipo akulakalaka mukadakhala osakhulupirira (kuti mufanane nawo). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 60

لَن تَنفَعَكُمۡ أَرۡحَامُكُمۡ وَلَآ أَوۡلَٰدُكُمۡۚ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ يَفۡصِلُ بَيۡنَكُمۡۚ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرٞ

Abale anu ngakhale ana anu sadzakuthandizani tsiku la Qiyâma (Allah) adzaweruza (pakati panu), ndipo Allah akuona zimene mukuchita. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 60

قَدۡ كَانَتۡ لَكُمۡ أُسۡوَةٌ حَسَنَةٞ فِيٓ إِبۡرَٰهِيمَ وَٱلَّذِينَ مَعَهُۥٓ إِذۡ قَالُواْ لِقَوۡمِهِمۡ إِنَّا بُرَءَٰٓؤُاْ مِنكُمۡ وَمِمَّا تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ كَفَرۡنَا بِكُمۡ وَبَدَا بَيۡنَنَا وَبَيۡنَكُمُ ٱلۡعَدَٰوَةُ وَٱلۡبَغۡضَآءُ أَبَدًا حَتَّىٰ تُؤۡمِنُواْ بِٱللَّهِ وَحۡدَهُۥٓ إِلَّا قَوۡلَ إِبۡرَٰهِيمَ لِأَبِيهِ لَأَسۡتَغۡفِرَنَّ لَكَ وَمَآ أَمۡلِكُ لَكَ مِنَ ٱللَّهِ مِن شَيۡءٖۖ رَّبَّنَا عَلَيۡكَ تَوَكَّلۡنَا وَإِلَيۡكَ أَنَبۡنَا وَإِلَيۡكَ ٱلۡمَصِيرُ

Ndithu inu muli ndi chitsanzo chabwino cha (mtumiki) Ibrahim ndi amene adali naye pamene adawauza anzawo (osakhulupirira kuti): “Ndithu ife tapatukana nanu pamodzi ndi milungu yanu imene mukuipembedza kusiya Allah; takukanani, ndipo chidani ndi kusakondana zaonekera poyera pakati pa inu ndi ife mpaka muyaya, kufikira, mutakhulupirira mwa Allah mmodzi (inunso chitani chimodzimodzi, muwakane abale anu amene ali akafiri), kupatula mawu a Ibrahim pamene adamuuza tate wake (kuti): “Ndithu ndikupempherani chikhululuko. Palibe chimene ndingakutetezereni nacho kwa Allah (ngati mutamuphatikiza Allah ndi zina.”) E Mbuye wathu! Kwa Inu tatsamira. Ndipo kwa Inu tatembenukira ndiponso kobwerera nkwa Inu.[356] info

[356] Apa akutiuza kuti titsanzire zimene adachita tate wa Shariya amene ndi Ibrahima pamodzi ndi omtsatira ake pamene adadzipatula kwa makolo awo ndi abale awo omwe adali m’chipembedzo chonama. Msilamu amkonde Allah kuposa tate wake, ana ake, mkazi wake, chuma chake ndi thupi lake limene. Atsogoze zofuna za Allah asanachite china chilichonse. Akatero akhala kuti wakhulupilira Allah mwachoonadi.

التفاسير:

external-link copy
5 : 60

رَبَّنَا لَا تَجۡعَلۡنَا فِتۡنَةٗ لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ وَٱغۡفِرۡ لَنَا رَبَّنَآۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ

E Mbuye wathu! Musatichite kukhala mayeso kwa amene sadakhulupirire, tikhululukireni Mbuye wathu! Ndithu Inu, Ndinu Amphamvu zopambana ndiponso Anzeru zakuya. info
التفاسير: