[163] Iyi ndinkhani yoyamba ya munthu wopha mnzake. Ndipo amene adaphedwayu ndiye munthu woyamba kulawa imfa. Wopha mnzakeyo ataona kuti mnzake wafadi, iye adangoti kakasi, kusowa chochita naye. Tero adangomsenza kumsana nkumangozungilirazungulira naye, kuopa kubwera naye kunyumba kuti anzake angamdziwe kuti ndiye wamupha. Makolo awo adali Adam ndi Hava. Mwamwayi, khwangwala adatulukira nayamba kumenyana ndimnzake mpaka kumupha. Kenako namkwilira m’nthaka. Tsono naye uja wopha mnzake adatsanzira zomwe khwangwala adachita. Nakumba dzenje nkukwilira mnzakeyo. N.B! Munthu ncholengedwa chomalizira kudza pa dziko. Zidamtsogolera zolengedwa zonse ndi zaka miyandamiyanda.