[300] Ngati makolo onse awiri atalimbikira ndi mphamvu zawo zonse kuti iwe umukane Allah, kapena kuti umuphatikize ndi chinthu china chomwe nchosayenera kukhala Allah, usawamvere pa zimenezo, chifukwa chakuti palibe kugonjera cholengedwa polakwira Mlengi.
[301] Alipo ena pakati pa anthu amene amangonena ndi malirime awo okha kuti: “Takhulupilira Allah.” Koma mmodzi wawo akavutitsidwa chifukwa cha chikhulupiliro chakecho, amatuluka m’chipembedzomo. Ndipo masautso a anthu amati ndicho chifukwa chomwe chidawachotsetsa m’chipembedzocho. Komatu chilango cha Allah nchosafanana ndi chilango cha anthu. Chofunika kwa iwo nkupilira ndi kulimba mtima; osatekeseka ndi chilichonse ngakhale choononga moyo wawo.
[302] M’ndime iyi, Allah akumthondoza Mtumiki Wake, Muhammad (s.a.w) pomufotokozera kuti kusakhulupilira kwa anthu akowa sichinthu chachilendo. Nawonso amene adalipo kale adamtsutsa Nuh ngakhaie kuti adalalikira kwa nthawi yayitali mpaka chigumula chidawamiza onse. Nawonso anthu akowa aonongedwa monga momwe zidalili ndi anthu a Nuh. Choncho usatekeseke ndi kusakhulupilira kwawo.