કુરઆન મજીદના શબ્દોનું ભાષાંતર - ચિચેવા ભાષામાં અનુવાદ - ખાલિદ ઇબ્રાહિમ બૈતાલા

પેજ નંબર:close

external-link copy
49 : 2

وَإِذۡ نَجَّيۡنَٰكُم مِّنۡ ءَالِ فِرۡعَوۡنَ يَسُومُونَكُمۡ سُوٓءَ ٱلۡعَذَابِ يُذَبِّحُونَ أَبۡنَآءَكُمۡ وَيَسۡتَحۡيُونَ نِسَآءَكُمۡۚ وَفِي ذَٰلِكُم بَلَآءٞ مِّن رَّبِّكُمۡ عَظِيمٞ

Ndipo (kumbukirani) pamene tidakupulumutsani kwa anthu a Farawo, omwe amakuzunzani ndi chilango choipa; adali kuzinga (kupha) ana anu achimuna ndikuwasiya moyo achikazi. Ndipo m’zimenezo mudali mayeso aakulu ochokera kwa Mbuye wanu. info
التفاسير:

external-link copy
50 : 2

وَإِذۡ فَرَقۡنَا بِكُمُ ٱلۡبَحۡرَ فَأَنجَيۡنَٰكُمۡ وَأَغۡرَقۡنَآ ءَالَ فِرۡعَوۡنَ وَأَنتُمۡ تَنظُرُونَ

Ndipo (kumbukiraninso) pamene tidailekanitsa nyanja chifukwa cha inu (kuti muoloke pa mchenga wouma), potero tidakupulumutsani ndi kuwamiza anthu a Farawo (pamodzi ndi iye mwini) uku inu mukuona; (chomwe chidali chizizwa choonekera). info
التفاسير:

external-link copy
51 : 2

وَإِذۡ وَٰعَدۡنَا مُوسَىٰٓ أَرۡبَعِينَ لَيۡلَةٗ ثُمَّ ٱتَّخَذۡتُمُ ٱلۡعِجۡلَ مِنۢ بَعۡدِهِۦ وَأَنتُمۡ ظَٰلِمُونَ

(Kumbukiraninso) pamene tidamulonjeza Mûsa masiku makumi anayi (kuti tidzampatsa buku la Taurat patapita masiku makumi anayi pambuyo pa kupulumuka kwanu ndi kuonongeka kwa Farawo); kenako inu mudapembedza thole (mwana wa ng’ombe) pambuyo pake, (iye kulibe, atapita ku chipangano cha Mbuye wake). Ndipo inu muli ochita zoipa. info
التفاسير:

external-link copy
52 : 2

ثُمَّ عَفَوۡنَا عَنكُم مِّنۢ بَعۡدِ ذَٰلِكَ لَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ

Kenako tidakukhululukirani pambuyo pa zimenezo, kuti muthokoze (mtendere wa Allah). info
التفاسير:

external-link copy
53 : 2

وَإِذۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡفُرۡقَانَ لَعَلَّكُمۡ تَهۡتَدُونَ

Ndipo (kumbukiraninso) pamene Mûsa tidampatsa buku lolekanitsa choonadi ndi chonama kuti inu muongoke (polilingalira ndi kutsatira malamulo ake). info
التفاسير:

external-link copy
54 : 2

وَإِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوۡمِهِۦ يَٰقَوۡمِ إِنَّكُمۡ ظَلَمۡتُمۡ أَنفُسَكُم بِٱتِّخَاذِكُمُ ٱلۡعِجۡلَ فَتُوبُوٓاْ إِلَىٰ بَارِئِكُمۡ فَٱقۡتُلُوٓاْ أَنفُسَكُمۡ ذَٰلِكُمۡ خَيۡرٞ لَّكُمۡ عِندَ بَارِئِكُمۡ فَتَابَ عَلَيۡكُمۡۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلتَّوَّابُ ٱلرَّحِيمُ

Ndipo (kumbukiraninso) pamene Mûsa adanena kwa anthu ake kuti “E inu anthu anga! Ndithudi, inu mwadzichitira nokha zoipa pompembedza thole (mwana wa ng’ombe). Choncho lapani kwa Mlengi wanu, ndipo iphanani nokha (amene ali abwino aphe oipa). Kutero ndi bwino kwa inu pamaso pa Mlengi wanu.” Choncho (Allah) wavomera kulapa kwanu. Ndithudi, Iye Ngovomera kulapa mochuluka, Wachisoni chosatha. info
التفاسير:

external-link copy
55 : 2

وَإِذۡ قُلۡتُمۡ يَٰمُوسَىٰ لَن نُّؤۡمِنَ لَكَ حَتَّىٰ نَرَى ٱللَّهَ جَهۡرَةٗ فَأَخَذَتۡكُمُ ٱلصَّٰعِقَةُ وَأَنتُمۡ تَنظُرُونَ

Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene Mudati: “E iwe Mûsa!; Sitingakukhulupirire iwe mpaka timuone Allah masomphenya.” Ndipo nkokomo wa moto udakugwirani uku inu mukuona. info
التفاسير:

external-link copy
56 : 2

ثُمَّ بَعَثۡنَٰكُم مِّنۢ بَعۡدِ مَوۡتِكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ

Kenako tidakuukitsani ku imfa pambuyo pakufa kwanu, kuti muyamike. info
التفاسير:

external-link copy
57 : 2

وَظَلَّلۡنَا عَلَيۡكُمُ ٱلۡغَمَامَ وَأَنزَلۡنَا عَلَيۡكُمُ ٱلۡمَنَّ وَٱلسَّلۡوَىٰۖ كُلُواْ مِن طَيِّبَٰتِ مَا رَزَقۡنَٰكُمۡۚ وَمَا ظَلَمُونَا وَلَٰكِن كَانُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ يَظۡلِمُونَ

Ndipo tidakuphimbani ndi mthunzi wa mitambo (pamene mudali kuoloka chipululu cha mchenga), ndipo tidakutsitsirani Mana (zakumwa zotsekemera ngati uchi) ndi Salwa (zinziri), ndi kukuuzani: “Idyani zinthu zabwino izi zimene takupatsani.” Komatu sadatichitire Ife choipa koma adali kudzichitira okha zoipa. info
التفاسير: