Firo maanaaji al-quraan tedduɗo oo - Eggo e ɗemngal Ciiciiwa - Kaalid Ibrahiima Biitala.

external-link copy
164 : 3

لَقَدۡ مَنَّ ٱللَّهُ عَلَى ٱلۡمُؤۡمِنِينَ إِذۡ بَعَثَ فِيهِمۡ رَسُولٗا مِّنۡ أَنفُسِهِمۡ يَتۡلُواْ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتِهِۦ وَيُزَكِّيهِمۡ وَيُعَلِّمُهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡحِكۡمَةَ وَإِن كَانُواْ مِن قَبۡلُ لَفِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٍ

Ndithudi, Allah adawachitira ubwino waukulu okhulupirira powatumizira Mtumiki wochokera mwa iwo yemwe akuwawerengera ma Ayah ake (ndime zake) ndikuwayeretsa ndikuwaphunzitsa buku ndi (mawu a) nzeru. Ndithudi, kale adali mkusokera koonekera.[97] info

[97] Apa Allah akukumbutsa Asilamu za chisomo chomwe adawapatsa pakuwapatsa Mtumiki, pomwe Mtumikiyo asanawadzere iwo adali anthu osokera. Koma kupyolera mwa Mtumikiyo akhala olungama.

التفاسير: