Firo maanaaji al-quraan tedduɗo oo - Eggo e ɗemngal Ciiciiwa - Kaalid Ibrahiima Biitala.

external-link copy
159 : 3

فَبِمَا رَحۡمَةٖ مِّنَ ٱللَّهِ لِنتَ لَهُمۡۖ وَلَوۡ كُنتَ فَظًّا غَلِيظَ ٱلۡقَلۡبِ لَٱنفَضُّواْ مِنۡ حَوۡلِكَۖ فَٱعۡفُ عَنۡهُمۡ وَٱسۡتَغۡفِرۡ لَهُمۡ وَشَاوِرۡهُمۡ فِي ٱلۡأَمۡرِۖ فَإِذَا عَزَمۡتَ فَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱللَّهِۚ إِنَّ ٱللَّهَ يُحِبُّ ٱلۡمُتَوَكِّلِينَ

Chifukwa cha chifundo chochokera kwa Allah, uli woleza mtima kwa iwo, (iwe Mtumiki Muhammad {s.a.w}). Ndipo ukadakhala waukali, wouma mtima, ndithudi, akadakuthawa pamaso pako. Choncho akhululukire ndi kuwapemphera chikhululuko (kwa Allah); ndipo chita nawo upo pa zinthu. Ndipo ngati watsimikiza, tsamira kwa Allah (basi, ndi kuchita chimene watsimikiza kuchichita). Ndithudi, Allah amakonda oyadzamira Kwake (odalira Iye). info
التفاسير: