Firo maanaaji al-quraan tedduɗo oo - Eggo e ɗemngal Ciiciiwa - Kaalid Ibrahiima Biitala.

Tonngoode hello ngoo:close

external-link copy
14 : 27

وَجَحَدُواْ بِهَا وَٱسۡتَيۡقَنَتۡهَآ أَنفُسُهُمۡ ظُلۡمٗا وَعُلُوّٗاۚ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُفۡسِدِينَ

Ndipo adazitsutsa (zisonyezozo) mwachinyengo ndi modzikuza chikhalirecho mitima yawo idatsimikiza (kuti ndizoona zochokera kwa Allah); choncho, yang’ana adali bwanji malekezero a oononga! info
التفاسير:

external-link copy
15 : 27

وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا دَاوُۥدَ وَسُلَيۡمَٰنَ عِلۡمٗاۖ وَقَالَا ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي فَضَّلَنَا عَلَىٰ كَثِيرٖ مِّنۡ عِبَادِهِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Ndipo ndithu Daud ndi Sulaiman tidawapatsa nzeru (zazikulu; adayamika Allah) adati: “Kuyamikidwa konse kwabwino nkwa Allah Yemwe watichitira ubwino kuposa ambiri mwa akapolo ake okhulupirira.” info
التفاسير:

external-link copy
16 : 27

وَوَرِثَ سُلَيۡمَٰنُ دَاوُۥدَۖ وَقَالَ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ عُلِّمۡنَا مَنطِقَ ٱلطَّيۡرِ وَأُوتِينَا مِن كُلِّ شَيۡءٍۖ إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ ٱلۡفَضۡلُ ٱلۡمُبِينُ

Ndipo Sulaiman adalowa mmalo mwa Daud pa nzeru ndi uneneri ndipo (Sulaiman) adati: “E inu anthu! Ndithu taphunzitsidwa (mpaka tikudziwa) chiyankhulo cha mbalame, ndiponso tapatsidwa chilichonse; ndithu umenewu ndiubwino wopenyeka. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 27

وَحُشِرَ لِسُلَيۡمَٰنَ جُنُودُهُۥ مِنَ ٱلۡجِنِّ وَٱلۡإِنسِ وَٱلطَّيۡرِ فَهُمۡ يُوزَعُونَ

Ndipo adasonkhanitsidwa kwa Sulaiman ankhondo ake ochokera m’ziwanda, anthu ndi mbalame, ndipo adawandandika m’magulumagulu. info
التفاسير:

external-link copy
18 : 27

حَتَّىٰٓ إِذَآ أَتَوۡاْ عَلَىٰ وَادِ ٱلنَّمۡلِ قَالَتۡ نَمۡلَةٞ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّمۡلُ ٱدۡخُلُواْ مَسَٰكِنَكُمۡ لَا يَحۡطِمَنَّكُمۡ سُلَيۡمَٰنُ وَجُنُودُهُۥ وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ

Kufikira pamene adadza pachigwa chanyelere, nyelere idanena (kuuza zinzake): “E inu nyelere, lowani m’nyumba zanu poopa kuti angakupondeni Sulaiman ndi magulu ake ankhondo pomwe iwo sakudziwa (za inu).” info
التفاسير:

external-link copy
19 : 27

فَتَبَسَّمَ ضَاحِكٗا مِّن قَوۡلِهَا وَقَالَ رَبِّ أَوۡزِعۡنِيٓ أَنۡ أَشۡكُرَ نِعۡمَتَكَ ٱلَّتِيٓ أَنۡعَمۡتَ عَلَيَّ وَعَلَىٰ وَٰلِدَيَّ وَأَنۡ أَعۡمَلَ صَٰلِحٗا تَرۡضَىٰهُ وَأَدۡخِلۡنِي بِرَحۡمَتِكَ فِي عِبَادِكَ ٱلصَّٰلِحِينَ

Choncho adamwetulira, mosekelera chifukwa cha mawu ake aja (mawu a nyelere); ndipo (Sulaiman) adati: “E Mbuye wanga! Ndipatseni nyonga zakuti ndizithokozera mtendere wanu umene mwandidalitsa nawo pamodzi ndi makolo anga, ndi kuti ndizichita zabwino (zomwe) mukuziyanja; Kupyolera m’chifundo chanu, ndiponso ndilowetseni m’gulu la akapolo anu abwino.” info
التفاسير:

external-link copy
20 : 27

وَتَفَقَّدَ ٱلطَّيۡرَ فَقَالَ مَالِيَ لَآ أَرَى ٱلۡهُدۡهُدَ أَمۡ كَانَ مِنَ ٱلۡغَآئِبِينَ

Ndipo adayamba kuyendera mbalame, adati: “Kodi bwanji sindikumuona Huduhudu? Kapena ali m’gulu la amene pano palibe?” info
التفاسير:

external-link copy
21 : 27

لَأُعَذِّبَنَّهُۥ عَذَابٗا شَدِيدًا أَوۡ لَأَاْذۡبَحَنَّهُۥٓ أَوۡ لَيَأۡتِيَنِّي بِسُلۡطَٰنٖ مُّبِينٖ

“Ndithu ndimulanga chilango chokhwima, kapena ndimzinga (ndimdula khosi) pokhapokha andibweletsere umboni womveka (wosonyeza kuti adachoka pazifukwa zomveka).” info
التفاسير:

external-link copy
22 : 27

فَمَكَثَ غَيۡرَ بَعِيدٖ فَقَالَ أَحَطتُ بِمَا لَمۡ تُحِطۡ بِهِۦ وَجِئۡتُكَ مِن سَبَإِۭ بِنَبَإٖ يَقِينٍ

Choncho (Hudhud) sadakhalitse nthawi yaitali; ndipo adati (kwa Sulaiman): “Ndatulukira zomwe iwe sudazitulukire, ndipo ndakubweletsera nkhani yotsimikizika kuchokera ku Saba.” info
التفاسير: