ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمه‌ى چوایی - خالد ابراهیم بيتالا

At-Tîn

external-link copy
1 : 95

وَٱلتِّينِ وَٱلزَّيۡتُونِ

Ndikulumbilira mitengo ya Mkuyu ndi Zitona (pansi pa mitengo imeneyi Ibrahim ndi Nuh (Nowa) adapeza uneneri), info
التفاسير:

external-link copy
2 : 95

وَطُورِ سِينِينَ

Ndi phiri la Sinai (pamene Allah adamulankhulira Mûsa), info
التفاسير:

external-link copy
3 : 95

وَهَٰذَا ٱلۡبَلَدِ ٱلۡأَمِينِ

Ndiponso mzinda uwu (wolemekezeka) wamtendere; (Makka, womwe adapatsiridwa uneneri Muhammad) (s.a.w). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 95

لَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ فِيٓ أَحۡسَنِ تَقۡوِيمٖ

Palibe chikaiko, tamulenga munthu mkalengedwe kabwino, kolingana (ndipo ali ndi mbiri zabwino).[457] info

[457] M’gulu la nyama palibe yopambana kuposa munthu mkalengedwe ndi pa nzeru.

التفاسير:

external-link copy
5 : 95

ثُمَّ رَدَدۡنَٰهُ أَسۡفَلَ سَٰفِلِينَ

Pambuyo pake tamubwezera pansi kumposa wa pansi.[458] info

[458] Munthu ali ndi makhalidwe awiri: Ngati agwiritsa ntchito nzeru zake amaongoka ndipo amaiposa nyama ili yonse. Koma ngati sagwiritsa ntchito nzeru zake amasokera ndi kukhala wapansi kuposa nyama zonse.

التفاسير:

external-link copy
6 : 95

إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَلَهُمۡ أَجۡرٌ غَيۡرُ مَمۡنُونٖ

Kupatula amene akhulupirira ndikumachita zabwino, adzakhala nawo iwo malipiro osatha. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 95

فَمَا يُكَذِّبُكَ بَعۡدُ بِٱلدِّينِ

Tsono nchiyani chakuchititsa kuti ukanire kuuka ndi malipiro pambuyo (poona mphamvu zathu pa chilichonse)?[459] info

[459] (Ndime 7-8) Allah akuuza munthu kuti: Pambuyo podziwa kuti Allah ndi Yemwe adapanga zimenezo, ndi chiyani nanga chikumukaikitsa za tsiku la chiweruziro?

التفاسير:

external-link copy
8 : 95

أَلَيۡسَ ٱللَّهُ بِأَحۡكَمِ ٱلۡحَٰكِمِينَ

Kodi Allah si Muweruzi wa nzeru kuposa aweruzi onse? info
التفاسير: