[337] M’ndime iyi, Allah akutifotokozera kuti pa tsiku la chimaliziro padzakhala kukangana pakati pa atsogeleri ndi anthu otsogoleredwa. Izi zidzachitika pamene otsogoleredwa adzatsimikiza kuti atsogoleri awo amawasokeza; ankangowalangiza zachabe. Potero adzakhala ndi madandaulo aakulu chifukwa chotsatira anthu osokera. Komatu madandaulo oterewa sadzawapindulira chilichonse popeza mwayi udzakhala utatha kale. Choncho nkofunika kuti potsata mtsogoleri aliyense tiyambe taganizira komwe akunka nafe; tisangokokedwa ngati nyama pakuti Allah adatipatsa dalitso lanzeru. Choncho tigwiritse ntchito bwino nzeru tsoka lisanatigwere.