[98] Asilamu makumi asanu ndi awiri (70) ataphedwa ndi enanso ochuluka atavulazidwa pa nkhondo ija ya Uhudi, Mtumiki (s.a.w) adawalamula Asilamu pompo, uku ali ndimabalawo, kuti awatsate adaniwo. Ndipo adawatsatadi. Koma adaniwo atamva mphekesera kuti akuwatsata naganiza kuti akutsatidwa ndi chigulu cha nkhondo cha Asilamu chachikulu, osati gulu lonlija lomwe adalipatsa mavuto. Choncho adaliyatsa liwiro kuthawa. Ndipo Asilamuwo adabwerera pambuyo poyenda mtunda wautali kuwatsata adaniwo. Tero Allah adawatamanda Asilamuwa pakumvera kwawo kumeneko.