ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمه‌ى چوایی - خالد ابراهیم بيتالا

شماره صفحه:close

external-link copy
23 : 27

إِنِّي وَجَدتُّ ٱمۡرَأَةٗ تَمۡلِكُهُمۡ وَأُوتِيَتۡ مِن كُلِّ شَيۡءٖ وَلَهَا عَرۡشٌ عَظِيمٞ

“Ndithu ine ndapeza mkazi akuwalamulira (anthu a ku dziko la Saba), ndipo wapatsidwa chilichonse; ndiponso ali ndi chimpando chachifumu chachikulu.” info
التفاسير:

external-link copy
24 : 27

وَجَدتُّهَا وَقَوۡمَهَا يَسۡجُدُونَ لِلشَّمۡسِ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَزَيَّنَ لَهُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ أَعۡمَٰلَهُمۡ فَصَدَّهُمۡ عَنِ ٱلسَّبِيلِ فَهُمۡ لَا يَهۡتَدُونَ

“Ndampeza iye ndi anthu ake akulambira dzuwa kusiya Allah; ndipo satana wawakometsera zochita zawo zoipa; choncho wawatsekereza ku njira yolungama, tero sadaongoke.” info
التفاسير:

external-link copy
25 : 27

أَلَّاۤ يَسۡجُدُواْۤ لِلَّهِ ٱلَّذِي يُخۡرِجُ ٱلۡخَبۡءَ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَيَعۡلَمُ مَا تُخۡفُونَ وَمَا تُعۡلِنُونَ

“Kuti asamlambire Allah yemwe amatulutsa zobisika kumwamba ndi pansi; ndipo akudziwa zimene mukubisa ndi zimene muonetsa poyera.” info
التفاسير:

external-link copy
26 : 27

ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ رَبُّ ٱلۡعَرۡشِ ٱلۡعَظِيمِ۩

“Allah! Palibe wina wopembedzedwa mwachoona koma Iye basi; Mbuye wa Arsh (Mpando wachifumu) waukulu.” info
التفاسير:

external-link copy
27 : 27

۞ قَالَ سَنَنظُرُ أَصَدَقۡتَ أَمۡ كُنتَ مِنَ ٱلۡكَٰذِبِينَ

(Sulaiman) adati “Tiona ngati wanena zoona kapena ngati) uli m’gulu la onama.” info
التفاسير:

external-link copy
28 : 27

ٱذۡهَب بِّكِتَٰبِي هَٰذَا فَأَلۡقِهۡ إِلَيۡهِمۡ ثُمَّ تَوَلَّ عَنۡهُمۡ فَٱنظُرۡ مَاذَا يَرۡجِعُونَ

“Pita ndi kalata yangayi, kaiponye kwa iwo; kenako ukadzipatule kwa iwo (ukakhale pambali) ndi kuona momwe azikayankhira.” info
التفاسير:

external-link copy
29 : 27

قَالَتۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمَلَؤُاْ إِنِّيٓ أُلۡقِيَ إِلَيَّ كِتَٰبٞ كَرِيمٌ

(Mfumukazi) idati; “E inu nduna! Ndithu kalata yolemekezeka yaponyedwa kwa ine.” info
التفاسير:

external-link copy
30 : 27

إِنَّهُۥ مِن سُلَيۡمَٰنَ وَإِنَّهُۥ بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

“Yachokera kwa Sulaiman, ndipo mawu ake ndi awa: ‘Mdzina la Allah, Wachifundo chambiri, Wachisoni.’ info
التفاسير:

external-link copy
31 : 27

أَلَّا تَعۡلُواْ عَلَيَّ وَأۡتُونِي مُسۡلِمِينَ

‘Musadzikweze kwa ine, ndipo idzani kwa ine muli ogonjera malamulo anga.” info
التفاسير:

external-link copy
32 : 27

قَالَتۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمَلَؤُاْ أَفۡتُونِي فِيٓ أَمۡرِي مَا كُنتُ قَاطِعَةً أَمۡرًا حَتَّىٰ تَشۡهَدُونِ

(Mfumukazi idaonjezera) kunena: “E inu nduna! ndilangizeni pankhani yangayi; sindilamula kanthu mpaka inu mutandibwerera.” info
التفاسير:

external-link copy
33 : 27

قَالُواْ نَحۡنُ أُوْلُواْ قُوَّةٖ وَأُوْلُواْ بَأۡسٖ شَدِيدٖ وَٱلۡأَمۡرُ إِلَيۡكِ فَٱنظُرِي مَاذَا تَأۡمُرِينَ

(Nduna) zidati: “Ife ndife eni nyonga ndi eni kumenya nkhondo mwaukali; koma zonse zili ndi inu; choncho yang’anani mmene mungalamulire.” info
التفاسير:

external-link copy
34 : 27

قَالَتۡ إِنَّ ٱلۡمُلُوكَ إِذَا دَخَلُواْ قَرۡيَةً أَفۡسَدُوهَا وَجَعَلُوٓاْ أَعِزَّةَ أَهۡلِهَآ أَذِلَّةٗۚ وَكَذَٰلِكَ يَفۡعَلُونَ

(Mfumukazi) idati: “Ndithu mafumu akamalowa m’mudzi (wa anthu), amauononga motheratu, ndi kuwachita olemekezeka a m’menemo kukhala onyozeka. Mmenemo ndimomwe amachitira (nthawi zonse).” info
التفاسير:

external-link copy
35 : 27

وَإِنِّي مُرۡسِلَةٌ إِلَيۡهِم بِهَدِيَّةٖ فَنَاظِرَةُۢ بِمَ يَرۡجِعُ ٱلۡمُرۡسَلُونَ

“Koma ine nditumiza mitulo kwa iwo ndi kuyembekezera zimene abwere nazo otumidwawo.” info
التفاسير: