[229] Dyera loipa kwambiri ndiko kunena koti: “Tandisiyani ndichite machimo, kenako ndidzalapa.” Dziwani kuti machimo omwe Allah angawakhululuke ngomwe munthu wawachita mosazindikira kapena kuti popanda kuwafunafuna, osati owachita mwadaladala ncholinga choti adzalapa pambuyo pake monga momwe abale ake a Yusuf ankaganizira.