ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمه‌ى چوایی - خالد ابراهیم بيتالا

Al-Qâri’ah

external-link copy
1 : 101

ٱلۡقَارِعَةُ

Kugunda kwa phokoso (la Qiyâma)! info
التفاسير:

external-link copy
2 : 101

مَا ٱلۡقَارِعَةُ

Kodi kugunda kwa phokosolo ndi chiyani? info
التفاسير:

external-link copy
3 : 101

وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا ٱلۡقَارِعَةُ

Ndichiyani chingakudziwitse za kugunda kwa phokoso (la Qiyâma komwe kudzawakomole anthu)? info
التفاسير:

external-link copy
4 : 101

يَوۡمَ يَكُونُ ٱلنَّاسُ كَٱلۡفَرَاشِ ٱلۡمَبۡثُوثِ

Limenelo ndi tsiku limene anthu adzakhala ngati agulugufe obalalika.[475] info

[475] Apa, pakutanthauza kuti anthu adzakhala ali balalabalala ngati agulugufe ndipo azidzangodziponya uku ndi uku, osadziwa kopita. Imeneyo ndi nthawi yotuluka m’manda.

التفاسير:

external-link copy
5 : 101

وَتَكُونُ ٱلۡجِبَالُ كَٱلۡعِهۡنِ ٱلۡمَنفُوشِ

Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya womwazidwa (wongouluka uku ndi uku mumlengalenga). info
التفاسير:

external-link copy
6 : 101

فَأَمَّا مَن ثَقُلَتۡ مَوَٰزِينُهُۥ

Tsono amene muyeso wake (wa zinthu zabwino) udzalemere (ndikupepuka zoipa).[476] info

[476] Tsiku limenelo ntchito zonse zabwino ndi zoipa zidzayesedwa ndi muyeso wa Allah, koma sitidadziwitsidwe kuti muyeso umenewo udzakhala wotani udzayesa zonse zazikulu ndi zazing’ono zomwe mpaka za mumtima.

التفاسير:

external-link copy
7 : 101

فَهُوَ فِي عِيشَةٖ رَّاضِيَةٖ

Ndiye kuti iye adzakhala mu umoyo wosangalatsa (patsiku la chiweruziro). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 101

وَأَمَّا مَنۡ خَفَّتۡ مَوَٰزِينُهُۥ

Ndipo yemwe muyeso wake (wa zinthu zabwino) udzapepuka (ndi kulemera zoipa), info
التفاسير:

external-link copy
9 : 101

فَأُمُّهُۥ هَاوِيَةٞ

Ndiye kuti mbuto yake ndi ku Hawiya. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 101

وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا هِيَهۡ

Kodi ndi chiyani chingakudziwitse za Hawiya? info
التفاسير:

external-link copy
11 : 101

نَارٌ حَامِيَةُۢ

Umenewo ndi Moto woyaka mwa ukali! info
التفاسير: