আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

Al-Insân

external-link copy
1 : 76

هَلۡ أَتَىٰ عَلَى ٱلۡإِنسَٰنِ حِينٞ مِّنَ ٱلدَّهۡرِ لَمۡ يَكُن شَيۡـٔٗا مَّذۡكُورًا

Ndithu munthu idampita nthawi yaitali kwambiri (asanauziridwe mzimu) pomwe sadali chinthu chotchulidwa. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 76

إِنَّا خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ مِن نُّطۡفَةٍ أَمۡشَاجٖ نَّبۡتَلِيهِ فَجَعَلۡنَٰهُ سَمِيعَۢا بَصِيرًا

Ndithu Ife tamlenga munthu kuchokera ku mbewu ya munthu yosakanikirana (ya mkazi ndi ya mwamuna) kuti timuyese mayeso (ndi malamulo Athu); choncho tidampanga kukhala wakumva ndi wopenya; (amve mawu a Allah ndi kuti aone zisonyezo Zake). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 76

إِنَّا هَدَيۡنَٰهُ ٱلسَّبِيلَ إِمَّا شَاكِرٗا وَإِمَّا كَفُورًا

Ndithu Ife tidamlongosolera njira yoongoka: kukhala wokhulupirira kapena wotsutsa (Zonse zili kwa iye). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 76

إِنَّآ أَعۡتَدۡنَا لِلۡكَٰفِرِينَ سَلَٰسِلَاْ وَأَغۡلَٰلٗا وَسَعِيرًا

Ndithu Ife okana tawakonzera unyolo (wam’miyendo yawo) ndi magoli (am’manja ndi m’makosi awo) ndi Moto waukali woyaka. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 76

إِنَّ ٱلۡأَبۡرَارَ يَشۡرَبُونَ مِن كَأۡسٖ كَانَ مِزَاجُهَا كَافُورًا

Ndithu ochita zabwino adzamwa vinyo, chosakanizira chake chidzakhala (madzi a) kaafura. info
التفاسير: