আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

পৃষ্ঠা নং:close

external-link copy
5 : 63

وَإِذَا قِيلَ لَهُمۡ تَعَالَوۡاْ يَسۡتَغۡفِرۡ لَكُمۡ رَسُولُ ٱللَّهِ لَوَّوۡاْ رُءُوسَهُمۡ وَرَأَيۡتَهُمۡ يَصُدُّونَ وَهُم مُّسۡتَكۡبِرُونَ

Kukanenedwa kwa iwo kuti: “Bwerani, akupemphereni chikhululuko mthenga wa Allah, akutembenuza mitu yawo (monyoza ndi modzitukumula), ndipo uwaona akunyoza uku akudzikweza (osatsatira langizo).” info
التفاسير:

external-link copy
6 : 63

سَوَآءٌ عَلَيۡهِمۡ أَسۡتَغۡفَرۡتَ لَهُمۡ أَمۡ لَمۡ تَسۡتَغۡفِرۡ لَهُمۡ لَن يَغۡفِرَ ٱللَّهُ لَهُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلۡفَٰسِقِينَ

Kwa iwowa nchimodzimodzi kuwapemphera kwako chikhululuko, kapena kusawapemphera. Allah sangawakhululukire (chifukwa cha kuzama kwawo m’kusakhulupirira). Ndithu Allah saongola anthu otuluka m’chilamulo (Chake). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 63

هُمُ ٱلَّذِينَ يَقُولُونَ لَا تُنفِقُواْ عَلَىٰ مَنۡ عِندَ رَسُولِ ٱللَّهِ حَتَّىٰ يَنفَضُّواْۗ وَلِلَّهِ خَزَآئِنُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَلَٰكِنَّ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ لَا يَفۡقَهُونَ

Amenewa ndiwo omwe akunena kwa Answari; (Asilamu aku Madina, kuti): “Musawapatse chuma (chanu) amene ali ndi Mtumiki wa Allah kuti abalalikane.” Pomwe nkhokwe zonse (zachuma) za kumwamba ndi dziko lapansi zili m’manja mwa Allah (ndipo amachipereka kwa amene wamfuna); koma achiphamaso sakuzindikira (zimenezo).[364] info

[364] (Ndime 7-8) Chifukwa chomwe ndime izi zidavumbulutsidwira ndi kuti tsiku lina Mtumiki (s.a.w) pomwe adali ndi gulu lake la nkhondo, munthu wina wa m’madera am’midzi adakangana ndi Msilamu wa mu mzinda wa Madina chifukwa cha madzi. Ndipo Mwarabu wa kumudzi uja adamenya Msilamu wa m’Madina ndi thabwa. Poona izi Msilamu wa ku Madina adapita kukasuma kwa mwana wa Ubayye amene adali munafiki (wachinyengo). Mwana wa Ubayyeyo adamuuza wosumayo kuti: “Musamawapatse chakudya omwe ali ndi Muhammad kuti abalalikane, athawe njala ndi kumsiya yekha Muhammad (s.a.w).” Adatinso: “Tikabwerera ku mzinda wa Madina, wolemekezeka adzatulutsa wonyozeka.” Apa amatanthauza kuti wolemekezeka ndiye iye, ndipo wonyozeka ndi Mtumiki Muhammad (s.a.w). Ndipo Allah adamuyankha ponena kuti: “Kulemekezeka ndi kwa Allah ndi Mthenga wake ndi okhulupilira; koma anthu achiphamaso sakudziwa zimenezi.”

التفاسير:

external-link copy
8 : 63

يَقُولُونَ لَئِن رَّجَعۡنَآ إِلَى ٱلۡمَدِينَةِ لَيُخۡرِجَنَّ ٱلۡأَعَزُّ مِنۡهَا ٱلۡأَذَلَّۚ وَلِلَّهِ ٱلۡعِزَّةُ وَلِرَسُولِهِۦ وَلِلۡمُؤۡمِنِينَ وَلَٰكِنَّ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ لَا يَعۡلَمُونَ

Akunena kuti: “Ngati tibwerera ku Madina wolemekezeka adzatulutsa wonyozeka m’menemo. “Pomwe ulemelero ngwa Allah ndi Mthenga Wake ndi okhulupirira; koma achinyengo sakudziwa (zimenezo).” info
التفاسير:

external-link copy
9 : 63

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تُلۡهِكُمۡ أَمۡوَٰلُكُمۡ وَلَآ أَوۡلَٰدُكُمۡ عَن ذِكۡرِ ٱللَّهِۚ وَمَن يَفۡعَلۡ ذَٰلِكَ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡخَٰسِرُونَ

E inu amene mwakhulupirira! Chuma chanu ngakhalenso ana anu zisakutangwanitseni ndi kusiya kukumbukira Allah (ndi kukwaniritsa zimene wakulamulani). Ndipo amene achite zimenezo iwo ndi otaika. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 63

وَأَنفِقُواْ مِن مَّا رَزَقۡنَٰكُم مِّن قَبۡلِ أَن يَأۡتِيَ أَحَدَكُمُ ٱلۡمَوۡتُ فَيَقُولَ رَبِّ لَوۡلَآ أَخَّرۡتَنِيٓ إِلَىٰٓ أَجَلٖ قَرِيبٖ فَأَصَّدَّقَ وَأَكُن مِّنَ ٱلصَّٰلِحِينَ

Perekani (mwachangu pa njira ya Allah) zina mwa zomwe takupatsani, isanamfikire mmodzi wa inu imfa (mwadzidzidzi) ndi kuyamba kunena (modandaula): “Mbuye wanga! Bwanji osandichedwetsa nthawi pang’ono kuti ndipereke sadaka (ndi kuti ndikonze zina zimene sindinazikwaniritse) ndi kutinso ndikhale mwa anthu anu abwino.” info
التفاسير:

external-link copy
11 : 63

وَلَن يُؤَخِّرَ ٱللَّهُ نَفۡسًا إِذَا جَآءَ أَجَلُهَاۚ وَٱللَّهُ خَبِيرُۢ بِمَا تَعۡمَلُونَ

Ndipo Allah sangauchedwetse mzimu (ngakhale ndi mphindi imodzi) ukaidzera nthawi yake ya imfa; ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene mukuchita, (ndipo adzakulipirani pa zimenezo). info
التفاسير: