[355] Inu Asilamu amene mwakhulupilira mwa Allah ndi Mthenga Wake (s.a.w) musawachite makafiri amene ndi adani anga ndiponso adani anu kukhala okondedwa anu ndi abwenzi anu. Chisonyezo cha chikhulupiliro kwa Msilamu ndiko kuwada adani a Allah, osati kuwakonda ndi kupalana nawo ubwenzi.
[356] Apa akutiuza kuti titsanzire zimene adachita tate wa Shariya amene ndi Ibrahima pamodzi ndi omtsatira ake pamene adadzipatula kwa makolo awo ndi abale awo omwe adali m’chipembedzo chonama. Msilamu amkonde Allah kuposa tate wake, ana ake, mkazi wake, chuma chake ndi thupi lake limene. Atsogoze zofuna za Allah asanachite china chilichonse. Akatero akhala kuti wakhulupilira Allah mwachoonadi.
[357] Allah sakutiletsa kuwachitira zabwino anthu amene sali Asilamu, mmalo mwake akutilamula kuti tiwachitire zabwino ngati alibe upandu uliwonse ndi Asilamu.