আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

Al-Qamar

external-link copy
1 : 54

ٱقۡتَرَبَتِ ٱلسَّاعَةُ وَٱنشَقَّ ٱلۡقَمَرُ

Nthawi ya chimaliziro (Qiyâma) yayandikira ndipo mwezi wagawikana. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 54

وَإِن يَرَوۡاْ ءَايَةٗ يُعۡرِضُواْ وَيَقُولُواْ سِحۡرٞ مُّسۡتَمِرّٞ

Koma akaona chozizwitsa akunyoza ndi kunena kuti: “Awa ndi matsenga womkeramkera patsogolo.” info
التفاسير:

external-link copy
3 : 54

وَكَذَّبُواْ وَٱتَّبَعُوٓاْ أَهۡوَآءَهُمۡۚ وَكُلُّ أَمۡرٖ مُّسۡتَقِرّٞ

Ndipo adatsutsa (choonadi) ndi kutsatira zilakolako (zawo zoipa) koma chinthu chilichonse (cha Allah) nchokhazikika. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 54

وَلَقَدۡ جَآءَهُم مِّنَ ٱلۡأَنۢبَآءِ مَا فِيهِ مُزۡدَجَرٌ

Ndipo ndithu zidawafika nkhani zomwe zili zokwanira kuwaopseza. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 54

حِكۡمَةُۢ بَٰلِغَةٞۖ فَمَا تُغۡنِ ٱلنُّذُرُ

Nzeru zokwana koma machenjezo (kwa iwo) sanawathandize. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 54

فَتَوَلَّ عَنۡهُمۡۘ يَوۡمَ يَدۡعُ ٱلدَّاعِ إِلَىٰ شَيۡءٖ نُّكُرٍ

Choncho, apewe (iwe Mtumiki) osakhulupirira, (yembekezani) tsiku loitana woitana (wa Allah) ku chinthu chovuta kwambiri, (chodedwa ndi mitima). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 54

خُشَّعًا أَبۡصَٰرُهُمۡ يَخۡرُجُونَ مِنَ ٱلۡأَجۡدَاثِ كَأَنَّهُمۡ جَرَادٞ مُّنتَشِرٞ

Maso awo ali zyoli chifukwa chakuopsa; adzatuluka m’manda uku ali ngati dzombe lobalalika (chifukwa cha kuchuluka), info
التفاسير:

external-link copy
8 : 54

مُّهۡطِعِينَ إِلَى ٱلدَّاعِۖ يَقُولُ ٱلۡكَٰفِرُونَ هَٰذَا يَوۡمٌ عَسِرٞ

Akuthamangira kwa woitana (uku atatukula mitu yawo, osatha kucheukira kwina). Adzanena osakhulupirira (tsiku lachiweruziro): “Ili nditsiku lovuta kwambiri.” info
التفاسير:

external-link copy
9 : 54

۞ كَذَّبَتۡ قَبۡلَهُمۡ قَوۡمُ نُوحٖ فَكَذَّبُواْ عَبۡدَنَا وَقَالُواْ مَجۡنُونٞ وَٱزۡدُجِرَ

Patsogolo pawo (Aquraishi) anthu a Nuh nawo adatsutsa, adamtsutsa kapolo Wathu nanena kuti: “Uyu ngwamisala!” Ndipo adaopsezedwa (ndi kuzunzidwa ndi mazunzo osiyanasiyana). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 54

فَدَعَا رَبَّهُۥٓ أَنِّي مَغۡلُوبٞ فَٱنتَصِرۡ

(Nuh) adaitana Mbuye wake (nati): “Ine ndagonjetsedwa (ndi anthu anga); choncho ndipulumutseni (kwa iwo).” info
التفاسير:

external-link copy
11 : 54

فَفَتَحۡنَآ أَبۡوَٰبَ ٱلسَّمَآءِ بِمَآءٖ مُّنۡهَمِرٖ

Tero tidatsekula makomo akumwamba ndi madzi otsika mopitiriza, mwamphamvu. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 54

وَفَجَّرۡنَا ٱلۡأَرۡضَ عُيُونٗا فَٱلۡتَقَى ٱلۡمَآءُ عَلَىٰٓ أَمۡرٖ قَدۡ قُدِرَ

Ndipo tidaing’amba nthaka kukhala ndi akasupe (ofwamphuka madzi mwamphamvu). Choncho adakumana madzi (akumwamba ndi am’nthaka kuti awaononge) pamuyeso wopimidwa ndi kulamulidwa (ndi Allah). info
التفاسير:

external-link copy
13 : 54

وَحَمَلۡنَٰهُ عَلَىٰ ذَاتِ أَلۡوَٰحٖ وَدُسُرٖ

Ndipo tidamnyamula Nuh pa chombo chamatabwa chokhomedwa ndi misomali (yamitengo). info
التفاسير:

external-link copy
14 : 54

تَجۡرِي بِأَعۡيُنِنَا جَزَآءٗ لِّمَن كَانَ كُفِرَ

Chinkayandama pamadzi ndi kuyang’aniridwa ndi Ife. Iyi ndi mphoto ya (Nuh) yemwe adakanidwa ndi anthu ake. info
التفاسير:

external-link copy
15 : 54

وَلَقَد تَّرَكۡنَٰهَآ ءَايَةٗ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٖ

Ndipo ndithu tidachisiya (chigumula) kukhala phunziro (pakuonongeka kwa osakhulupirira ndi kupulumuka kwa okhulupirira). Kodi alipo wolikumbukira (ndi kupeza nalo malango abwino?) info
التفاسير:

external-link copy
16 : 54

فَكَيۡفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ

Kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa onyoza!) info
التفاسير:

external-link copy
17 : 54

وَلَقَدۡ يَسَّرۡنَا ٱلۡقُرۡءَانَ لِلذِّكۡرِ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٖ

Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an kuti ikhale chikumbutso. Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino?) info
التفاسير:

external-link copy
18 : 54

كَذَّبَتۡ عَادٞ فَكَيۡفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ

Âdi adamtsutsa (mneneri wawo Hud), kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa onyoza)! info
التفاسير:

external-link copy
19 : 54

إِنَّآ أَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ رِيحٗا صَرۡصَرٗا فِي يَوۡمِ نَحۡسٖ مُّسۡتَمِرّٖ

Ndithu Ife tidawatumizira mphepo yozizira, yaphokoso, m’tsiku latsoka lopitilira, info
التفاسير:

external-link copy
20 : 54

تَنزِعُ ٱلنَّاسَ كَأَنَّهُمۡ أَعۡجَازُ نَخۡلٖ مُّنقَعِرٖ

Idawazula anthu (kuchoka m’malo mwawo ndi kuwaponya panthaka ali akufa) ngati matsinde a mitengo yakanjedza ozulidwa m’malo mwake. info
التفاسير:

external-link copy
21 : 54

فَكَيۡفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ

Kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa onyoza)! info
التفاسير:

external-link copy
22 : 54

وَلَقَدۡ يَسَّرۡنَا ٱلۡقُرۡءَانَ لِلذِّكۡرِ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٖ

Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an kuti ikhale chikumbutso. Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino?) info
التفاسير:

external-link copy
23 : 54

كَذَّبَتۡ ثَمُودُ بِٱلنُّذُرِ

Asamudu adatsutsa machenjezo. info
التفاسير:

external-link copy
24 : 54

فَقَالُوٓاْ أَبَشَرٗا مِّنَّا وَٰحِدٗا نَّتَّبِعُهُۥٓ إِنَّآ إِذٗا لَّفِي ضَلَٰلٖ وَسُعُرٍ

Ndipo adati: “Kodi titsatire munthu mmodzi wochokera mwa ife? Ndithu ife ngati titamtsatira ndiye kuti tili nkusokera ndiponso misala.” info
التفاسير:

external-link copy
25 : 54

أَءُلۡقِيَ ٱلذِّكۡرُ عَلَيۡهِ مِنۢ بَيۡنِنَا بَلۡ هُوَ كَذَّابٌ أَشِرٞ

Kodi am’vumbulutsira iye chikumbutso pakati pathu, (pomwe tili nawo oposa iye pa ulemelero)? Koma iye ndiwabodza ndi wodzitukumu.” info
التفاسير:

external-link copy
26 : 54

سَيَعۡلَمُونَ غَدٗا مَّنِ ٱلۡكَذَّابُ ٱلۡأَشِرُ

Mawa lino adzadziwa (tsiku lakuwatsikira chilango,) kuti ndiyani wabodza wodzitukumula (iwo kapena Swaleh). info
التفاسير:

external-link copy
27 : 54

إِنَّا مُرۡسِلُواْ ٱلنَّاقَةِ فِتۡنَةٗ لَّهُمۡ فَٱرۡتَقِبۡهُمۡ وَٱصۡطَبِرۡ

(Tidamuuza mneneriyo kuti) ndithu Ife titumiza ngamira yaikazi kuti ikhale mayeso kwa iwo. Choncho adikire, ndipo pirira. info
التفاسير:

external-link copy
28 : 54

وَنَبِّئۡهُمۡ أَنَّ ٱلۡمَآءَ قِسۡمَةُۢ بَيۡنَهُمۡۖ كُلُّ شِرۡبٖ مُّحۡتَضَرٞ

Ndipo auze kuti madzi agawidwa pakati pawo (ndi ngamira). Aliyense ali ndi tsiku lopita kukatunga. info
التفاسير:

external-link copy
29 : 54

فَنَادَوۡاْ صَاحِبَهُمۡ فَتَعَاطَىٰ فَعَقَرَ

Koma adaitana mnzawo (wa mphulupulu). Choncho adakonzeka kupha ngamirayo ndipo adaipha. info
التفاسير:

external-link copy
30 : 54

فَكَيۡفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ

Kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa anthu otsutsa)! info
التفاسير:

external-link copy
31 : 54

إِنَّآ أَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ صَيۡحَةٗ وَٰحِدَةٗ فَكَانُواْ كَهَشِيمِ ٱلۡمُحۡتَظِرِ

Ndithu tidawatumizira nkuwe umodzi choncho adakhala ngati udzu ndi mitengo youma yaomanga khola. info
التفاسير:

external-link copy
32 : 54

وَلَقَدۡ يَسَّرۡنَا ٱلۡقُرۡءَانَ لِلذِّكۡرِ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٖ

Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an kuti ikhale chikumbutso. Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino?) info
التفاسير:

external-link copy
33 : 54

كَذَّبَتۡ قَوۡمُ لُوطِۭ بِٱلنُّذُرِ

Anthu a Luti adatsutsa machenjezo (a mneneri wawo). info
التفاسير:

external-link copy
34 : 54

إِنَّآ أَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ حَاصِبًا إِلَّآ ءَالَ لُوطٖۖ نَّجَّيۡنَٰهُم بِسَحَرٖ

Ndithu Ife tidawatumizira chimphepo champhamvu choulutsa miyala (ndi kuwagenda), kupatula akubanja la Luti; tidawapulumutsa (ku chilangocho) m’bandakucha, info
التفاسير:

external-link copy
35 : 54

نِّعۡمَةٗ مِّنۡ عِندِنَاۚ كَذَٰلِكَ نَجۡزِي مَن شَكَرَ

(Choncho kupulumukako kudali) chisomo chochokera kwa Ife (pa iwo). Momwemo ndimo timamlipirira wothokoza. info
التفاسير:

external-link copy
36 : 54

وَلَقَدۡ أَنذَرَهُم بَطۡشَتَنَا فَتَمَارَوۡاْ بِٱلنُّذُرِ

Ndipo ndithu (Luti) adawachenjeza anthu ake za kulanga Kwathu koopsa. Koma adakaikira machenjezo (ake ndi kumtsutsa). info
التفاسير:

external-link copy
37 : 54

وَلَقَدۡ رَٰوَدُوهُ عَن ضَيۡفِهِۦ فَطَمَسۡنَآ أَعۡيُنَهُمۡ فَذُوقُواْ عَذَابِي وَنُذُرِ

Ndipo ndithu adafuna kwa iye kuti awapatse alendo ake (kuti achite nawo zauve), koma tidafafaniza maso awo (kuti ikhale mphoto pa zimene adafunazo). (Ndipo tidawauza): “Choncho lawani chilango Changa ndi machenjezo Anga.” info
التفاسير:

external-link copy
38 : 54

وَلَقَدۡ صَبَّحَهُم بُكۡرَةً عَذَابٞ مُّسۡتَقِرّٞ

Ndipo ndithu chidawadzera mwadzidzidzi chilango chokhazikika, nthawi yam’mamawa. info
التفاسير:

external-link copy
39 : 54

فَذُوقُواْ عَذَابِي وَنُذُرِ

Choncho (kudanenedwa kwa iwo) “Lawani chilango Changa ndi machenjezo Anga.” info
التفاسير:

external-link copy
40 : 54

وَلَقَدۡ يَسَّرۡنَا ٱلۡقُرۡءَانَ لِلذِّكۡرِ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٖ

Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an (kuti ikhale chikumbutso). Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino)? info
التفاسير:

external-link copy
41 : 54

وَلَقَدۡ جَآءَ ءَالَ فِرۡعَوۡنَ ٱلنُّذُرُ

Ndipo ndithu machenjezo (ondondozana) adawadzera anthu a Farawo (ndi iye mwini). info
التفاسير:

external-link copy
42 : 54

كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا كُلِّهَا فَأَخَذۡنَٰهُمۡ أَخۡذَ عَزِيزٖ مُّقۡتَدِرٍ

Adatsutsa zozizwitsa Zathu zonse (zimene zidadza kupyolera m’manja mwa aneneri Athu). Choncho tidawalanga, kulanga kwa Wamphamvu (Wosapambanidwa), Wokhoza. info
التفاسير:

external-link copy
43 : 54

أَكُفَّارُكُمۡ خَيۡرٞ مِّنۡ أُوْلَٰٓئِكُمۡ أَمۡ لَكُم بَرَآءَةٞ فِي ٱلزُّبُرِ

Kodi osakhulupirira anuwa ndi abwino kuposa iwo (kotero kuti sadzaonongedwa)? Kapena zalembedwa m’mabuku kuti inu mdzasiyidwa (sadzakuonongani monga momwe adawaonongera akale?) info
التفاسير:

external-link copy
44 : 54

أَمۡ يَقُولُونَ نَحۡنُ جَمِيعٞ مُّنتَصِرٞ

Kapena akunena kuti: “Ife ndiochuluka titha kudziteteza (palibe angatipambane)?” info
التفاسير:

external-link copy
45 : 54

سَيُهۡزَمُ ٱلۡجَمۡعُ وَيُوَلُّونَ ٱلدُّبُرَ

(Auze): Gululo ligonjetsedwa ndipo athawa ndi kutembenuza misana. info
التفاسير:

external-link copy
46 : 54

بَلِ ٱلسَّاعَةُ مَوۡعِدُهُمۡ وَٱلسَّاعَةُ أَدۡهَىٰ وَأَمَرُّ

Koma lonjezo la chilango chawo ndi tsiku la chiweruziro, ndipo tsiku la chiweruziro ndi latsoka lalikulu, lowawa kwabasi (kwa osakhulupirira). info
التفاسير:

external-link copy
47 : 54

إِنَّ ٱلۡمُجۡرِمِينَ فِي ضَلَٰلٖ وَسُعُرٖ

Ndithu oipa (mwa awa ndi aja) ali nkusokera ndi misala. info
التفاسير:

external-link copy
48 : 54

يَوۡمَ يُسۡحَبُونَ فِي ٱلنَّارِ عَلَىٰ وُجُوهِهِمۡ ذُوقُواْ مَسَّ سَقَرَ

Tsiku limene adzakokedwera ku Moto ndi nkhope zawo, (kudzanenedwa kwa iwo:) “Lawani zowawa za Jahena (ndi kutentha kwake)! info
التفاسير:

external-link copy
49 : 54

إِنَّا كُلَّ شَيۡءٍ خَلَقۡنَٰهُ بِقَدَرٖ

Ndithu Ife tachilenga chinthu chilichonse ndi muyeso (kulingana ndi zolinga). info
التفاسير:

external-link copy
50 : 54

وَمَآ أَمۡرُنَآ إِلَّا وَٰحِدَةٞ كَلَمۡحِۭ بِٱلۡبَصَرِ

Ndipo silili lamulo Lathu (pa chinthu tikachifuna) koma liwu limodzi, (timangoti kwa chinthucho: “Chitika.” Ndipo chimachitika mwachangu) ngati kuphethira kwa diso. info
التفاسير:

external-link copy
51 : 54

وَلَقَدۡ أَهۡلَكۡنَآ أَشۡيَاعَكُمۡ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٖ

Ndipo ndithu tidawaononga anzanu (onga inu osakhulupirira): Kodi alipo wokumbuka? info
التفاسير:

external-link copy
52 : 54

وَكُلُّ شَيۡءٖ فَعَلُوهُ فِي ٱلزُّبُرِ

Ndipo chinthu chilichonse adachichita iwowo (pa dziko lapansi) chili mkaundula. info
التفاسير:

external-link copy
53 : 54

وَكُلُّ صَغِيرٖ وَكَبِيرٖ مُّسۡتَطَرٌ

Ndipo ntchito iliyonse, yaing’ono kapena yaikulu, idalembedwa; (palibe chimene chingamsowe). info
التفاسير:

external-link copy
54 : 54

إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي جَنَّٰتٖ وَنَهَرٖ

Ndithu oopa Allah adzakhala m’Minda ya ulemelero waukulu ndi Mitsinje (yosiyanasiyana). info
التفاسير:

external-link copy
55 : 54

فِي مَقۡعَدِ صِدۡقٍ عِندَ مَلِيكٖ مُّقۡتَدِرِۭ

Pokhala pabwino pachoonadi, (popanda mawu achabe ndi machimo), kwa Mfumu yokhoza chilichonse. info
التفاسير: