আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

Al-Jâthiyah

external-link copy
1 : 45

حمٓ

Hâ-Mîm. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 45

تَنزِيلُ ٱلۡكِتَٰبِ مِنَ ٱللَّهِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡحَكِيمِ

Chivumbulutso cha buku (ili) chochokera kwa Allah Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 45

إِنَّ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ لَأٓيَٰتٖ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ

Ndithu kuthambo ndi m’nthaka muli zisonyezo (zazikulu zosonyeza kuti Allah alipo) kwa okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 45

وَفِي خَلۡقِكُمۡ وَمَا يَبُثُّ مِن دَآبَّةٍ ءَايَٰتٞ لِّقَوۡمٖ يُوقِنُونَ

Ndiponso mkalengedwe kanu ndi zimene wazifalitsa mmenemo, mu zamoyo ndizisonyezo kwa anthu amene akutsimikiza. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 45

وَٱخۡتِلَٰفِ ٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِ وَمَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مِن رِّزۡقٖ فَأَحۡيَا بِهِ ٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ مَوۡتِهَا وَتَصۡرِيفِ ٱلرِّيَٰحِ ءَايَٰتٞ لِّقَوۡمٖ يَعۡقِلُونَ

Ndi kusinthana kwa usana ndi usiku, ndi mvula imene Allah akutsitsa kuchokera kumwamba, akuukitsa nthaka ndi mvulayo, itafa (itauma), ndi kuyendetsa mphepo mosinthasintha; (zonsezi) ndi zisonyezo kwa anthu anzeru. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 45

تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱللَّهِ نَتۡلُوهَا عَلَيۡكَ بِٱلۡحَقِّۖ فَبِأَيِّ حَدِيثِۭ بَعۡدَ ٱللَّهِ وَءَايَٰتِهِۦ يُؤۡمِنُونَ

Izi ndi Ayah (ndime) za Allah; tikukuwerengera iwe mwachoonadi. Kodi ndi nkhani yanji adzaikhulupirire atapanda kulabadira nkhani ya Allah ndi Ayah Zake? info
التفاسير:

external-link copy
7 : 45

وَيۡلٞ لِّكُلِّ أَفَّاكٍ أَثِيمٖ

Kuonongeka kuli pa aliyense wopeka zinthu, wamachimo ambiri. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 45

يَسۡمَعُ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِ ثُمَّ يُصِرُّ مُسۡتَكۡبِرٗا كَأَن لَّمۡ يَسۡمَعۡهَاۖ فَبَشِّرۡهُ بِعَذَابٍ أَلِيمٖ

Amene akumva Ayah za Allah zikuwerengedwa kwa iye kenako nkumapitiriza (zochita zake zosalungama) uku akudzikweza ngati kuti sadazimve ayazo; muuze nkhani ya chilango chowawa. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 45

وَإِذَا عَلِمَ مِنۡ ءَايَٰتِنَا شَيۡـًٔا ٱتَّخَذَهَا هُزُوًاۚ أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ عَذَابٞ مُّهِينٞ

Ndipo akadziwa chinthu chochepa chochokera mma Ayah athu, amachichitira chipongwe; amenewa ndi amene adzakhala ndi chilango chosambula. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 45

مِّن وَرَآئِهِمۡ جَهَنَّمُۖ وَلَا يُغۡنِي عَنۡهُم مَّا كَسَبُواْ شَيۡـٔٗا وَلَا مَا ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ أَوۡلِيَآءَۖ وَلَهُمۡ عَذَابٌ عَظِيمٌ

Jahannam ili (kuwayembekezera) kuseri kwawo; ndipo zimene adachita sizidzawathandiza chilichonse, ngakhale atetezi amene adadzipangira kusiya Allah (sadzawathandiza); ndipo adzapeza chilango chachikulu. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 45

هَٰذَا هُدٗىۖ وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِمۡ لَهُمۡ عَذَابٞ مِّن رِّجۡزٍ أَلِيمٌ

Ichi ndi chiongoko; ndipo amene adakanira Ayah za Mbuye wawo, adzakhala ndi chilango chachikulu chochokera mchilango chowawa. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 45

۞ ٱللَّهُ ٱلَّذِي سَخَّرَ لَكُمُ ٱلۡبَحۡرَ لِتَجۡرِيَ ٱلۡفُلۡكُ فِيهِ بِأَمۡرِهِۦ وَلِتَبۡتَغُواْ مِن فَضۡلِهِۦ وَلَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ

Allah ndi Amene wakugonjetserani nyanja kuti zombo ziziyenda mmenemo mwa lamulo Lake; ndikuti munke mufunafuna chifundo Chake kuti muthokoze. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 45

وَسَخَّرَ لَكُم مَّا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِ جَمِيعٗا مِّنۡهُۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يَتَفَكَّرُونَ

Ndipo wakugonjetserani za kumwamba ndi zam’nthaka, zonse zikuchokera kwa Iye. Ndithu mzimenezo muli zisonyezo kwa anthu amene amalingalira. info
التفاسير: