আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

Yâ-Sîn

external-link copy
1 : 36

يسٓ

Yâ-Sîn. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 36

وَٱلۡقُرۡءَانِ ٱلۡحَكِيمِ

Ndikulumbira Qur’an (iyi yomwe yakonzedwa mwaluso) yodzazidwa ndi mawu anzeru. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 36

إِنَّكَ لَمِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ

Ndithu iwe (Muhammad {s.a.w}) ndimmodzi wa atumiki (amene Allah adawatuma kwa anthu kuti akawasonyeze chiongoko). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 36

عَلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ

(Uli) panjira yolunjika. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 36

تَنزِيلَ ٱلۡعَزِيزِ ٱلرَّحِيمِ

(Qur’an iyi) nchivumbulutso cha Mwini Mphamvu zoposa; (palibe chokanika kwa Iye) Wachisoni chosatha. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 36

لِتُنذِرَ قَوۡمٗا مَّآ أُنذِرَ ءَابَآؤُهُمۡ فَهُمۡ غَٰفِلُونَ

Kuti uwachenjeze anthu omwe makolo awo sadachenjezedwe; choncho iwo ngoiwala (zomwe zili zofunika kuchitira Allah ndi kudzichitira okha pamodzi ndi anthu ena). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 36

لَقَدۡ حَقَّ ٱلۡقَوۡلُ عَلَىٰٓ أَكۡثَرِهِمۡ فَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ

Ndithu mawu (onena za chilango) atsimikizika pa ambiri a iwo; poti iwo sakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 36

إِنَّا جَعَلۡنَا فِيٓ أَعۡنَٰقِهِمۡ أَغۡلَٰلٗا فَهِيَ إِلَى ٱلۡأَذۡقَانِ فَهُم مُّقۡمَحُونَ

Ndithu Ife taika magoli m’makosi mwawo ofika kuzibwano, kotero kuti mitu yawo yayang’ana mmwamba; (siingathe kutembenuka ndi kuyang’ana). info
التفاسير:

external-link copy
9 : 36

وَجَعَلۡنَا مِنۢ بَيۡنِ أَيۡدِيهِمۡ سَدّٗا وَمِنۡ خَلۡفِهِمۡ سَدّٗا فَأَغۡشَيۡنَٰهُمۡ فَهُمۡ لَا يُبۡصِرُونَ

Ndipo tawaikira chotsekereza patsogolo pawo ndi chotsekereza pambuyo pawo, ndipo (maso awo) tawaphimba, tero iwo saona (zapatsogolo ndi pambuyo pawo). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 36

وَسَوَآءٌ عَلَيۡهِمۡ ءَأَنذَرۡتَهُمۡ أَمۡ لَمۡ تُنذِرۡهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ

Ndipo kwa iwo nchimodzimodzi, uwachenjeze ngakhale usawachenjeze sangakhulupirire. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 36

إِنَّمَا تُنذِرُ مَنِ ٱتَّبَعَ ٱلذِّكۡرَ وَخَشِيَ ٱلرَّحۡمَٰنَ بِٱلۡغَيۡبِۖ فَبَشِّرۡهُ بِمَغۡفِرَةٖ وَأَجۡرٖ كَرِيمٍ

Ndithu kuchenjeza kwako kupindulira amene watsatira Qur’an ndi kumuopa (Allah) Wachifundo chambiri ngakhale sakumuona. Wotere muuze nkhani yabwino ya chikhululuko (chochokera kwa Allah pa machimo ake) ndi malipiro aulemu. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 36

إِنَّا نَحۡنُ نُحۡيِ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَنَكۡتُبُ مَا قَدَّمُواْ وَءَاثَٰرَهُمۡۚ وَكُلَّ شَيۡءٍ أَحۡصَيۡنَٰهُ فِيٓ إِمَامٖ مُّبِينٖ

Ndithu Ife tidzaukitsa akufa, ndipo tikulemba zimene atsogoza (m’dziko lapansi m’zochita zawo) ndi zomwe amasiya pambuyo (atafa, zonkerankera mtsogolo), ndipo chinthu chilichonse tachilemba m’kaundula wopenyeka (wofotokoza chilichonse). info
التفاسير: