আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

Al-’Adiy ât

external-link copy
1 : 100

وَٱلۡعَٰدِيَٰتِ ضَبۡحٗا

Ndikulumbilira akavalo othamanga ali ndi phuma, info
التفاسير:

external-link copy
2 : 100

فَٱلۡمُورِيَٰتِ قَدۡحٗا

Ndi otulutsa moto ku zikhotwa (pomenyetsa miyendo m’miyala), info
التفاسير:

external-link copy
3 : 100

فَٱلۡمُغِيرَٰتِ صُبۡحٗا

Ndi othira nkhondo adani mmawa (dzuwa lisadatuluke), info
التفاسير:

external-link copy
4 : 100

فَأَثَرۡنَ بِهِۦ نَقۡعٗا

Ndi kuulutsa fumbi lambiri (kwa adani) nthawi imeneyo, info
التفاسير:

external-link copy
5 : 100

فَوَسَطۡنَ بِهِۦ جَمۡعًا

Ndikulowelera mkatikati mwa adani. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 100

إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لِرَبِّهِۦ لَكَنُودٞ

Ndithu munthu ali wokanira Mbuye wake, (sathokoza Allah pa zimene amdalitsa nazo).[472] info

[472] Tanthauzo la “kukanira Mbuye wake” ndi kuukanira mtendere Wake. Ndipo kukanira mtendere ndiko kusagwiritsira ntchito mtenderewo mnjira zabwino, monga m’mapemphero ndi zina zotero.

التفاسير:

external-link copy
7 : 100

وَإِنَّهُۥ عَلَىٰ ذَٰلِكَ لَشَهِيدٞ

Ndithudi iye pa zimenezi ndi mboni (yodzichitira yekha kupyolera mzochitachita zake). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 100

وَإِنَّهُۥ لِحُبِّ ٱلۡخَيۡرِ لَشَدِيدٌ

Ndipo ndithu iye ndiwokonda chuma kwambiri (ndiponso ngwamsulizo).[473] info

[473] Kapena kuti ali wofunitsitsa chuma kwambiri; kumeneko ndikumangoti mtima dyokodyoko pachuma. Ukachipeza ndikumachichitira umbombo ndipo ndikumaganiza kuti chumacho nchopambana china chilichonse.

التفاسير:

external-link copy
9 : 100

۞ أَفَلَا يَعۡلَمُ إِذَا بُعۡثِرَ مَا فِي ٱلۡقُبُورِ

Kodi sakudziwa zikadzatulutsidwa za m’manda, info
التفاسير:

external-link copy
10 : 100

وَحُصِّلَ مَا فِي ٱلصُّدُورِ

Ndikudzasonkhanitsidwa ndi kuonekera poyera zomwe zidali m’mitima? info
التفاسير:

external-link copy
11 : 100

إِنَّ رَبَّهُم بِهِمۡ يَوۡمَئِذٖ لَّخَبِيرُۢ

Ndithu tsiku limenelo Mbuye wawo adzawadziwa kwambiri (ndikuwalongosolera zonse zochita zawo).[474] info

[474] “Kuwadziwa kwambiri,” kukutanthauza kuti Iye ngodziwa zazikuluzikulu ndi zazing’onozing’ono zoonekera poyera ndi zobisika. Tsiku limenelo adzawalipira chilichonse chimene adachita.

التفاسير: